Esr. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hamani achita chiwembu Ayuda

1Zitatha zimenezi, mfumu Ahasuwero adamkweza Hamani Mwagagi, mwana wa Amateta. Adamkuza ndi kumpatsa mpando wapamwamba, kupambana akulu onse amene anali naye pamodzi.

2Tsono atumiki onse a mfumu amene ankakhala pa chipata cha mfumu ankamugwadira ndi kumamuŵeramira mwaulemu Hamaniyo. Mfumu ndiyo idaalamula zimenezi. Koma Mordekai sankamugwadirako kapenanso kumuŵeramira.

3Apo atumiki a mfumu amene ankakhala pa chipata cha mfumu, adamufunsa Mordekai kuti, “Chifukwa chiyani ukuswa lamulo la mfumu?”

4Popeza kuti ankalankhula naye tsiku ndi tsiku, koma iyeyo osaŵamvera konse, iwo adauza Hamani kuti aone ngati Mordekai nkusintha mau ake, poti adaaŵauza kuti anali Myuda.

5Tsono Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira ngakhalenso kumuŵeramira, adapsa mtima kwambiri.

6Koma sadafune kupha Mordekai yekha. Anali atamva za anthu a mtundu wa Mordekai, tsono Hamaniyo adatsimikiza zoti aononge Ayuda onse, anthu a mtundu wa Mordekai, m'dziko lonse limene mfumu Ahasuwero ankalamulira.

7Pa mwezi woyamba, mwezi wa Nisani, chaka cha 12 cha ufumu wa Ahasuwero, anthu adaombeza ula wa Puri pamaso pa Hamaniyo, kuti adziŵe tsiku ndi mwezi wake woyenera, mpaka ula udagwa pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara.

8Tsono Hamani adauza mfumu Ahasuwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene udabalalika m'dziko lonseli, ndipo udamwazikira ku mitundu ya anthu m'madera onse amene inu mumalamulira. Malamulo ao ngosiyana ndi malamulo a anthu ena onse, ndipo anthuwo satsata malamulo a mfumu, kotero kuti si chinthu chaphindu kuti mfumu iŵalekerere.

9Zikakukomerani amfumu, mulamule kuti mtundu wonsewo uwonongedwe, ndipo ine ndidzapereka matani 345 a siliva m'manja mwa anthu oyang'anira ntchito ya mfumu, kuti aike ndalamazo m'matumba osungiramo chuma cha mfumu.”

10Pamenepo mfumu idavula mphete yosindikizira ya ku dzanja lake, nkuipereka kwa Hamani Mwagagi, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda.

11Kenaka mfumu idamuuza Hamaniyo kuti, “Ndalama nzako, pamodzi ndi anthu omwe, kuti uŵachite zimene zikukomere.”

12Tsono alembi a mfumu adaitanidwa pa tsiku la 13 la mwezi woyamba, ndipo adalemba kalata yosimba zonse zimene Hamani adaalamula. Adaitumiza kwa akalonga a mfumu ndi kwa akazembe a m'madera onse, ndi kwa akulu onse oyang'anira mitundu ya anthu, dziko lililonse kalata yakeyake, anthu a mtundu uliwonse m'chilankhulo chaochao. Kalatayo idalembedwa m'dzina la mfumu Ahasuwero, ndipo adaisindikiza ndi mphete yake.

13Makalatawo adaŵatumiza ndi anthu amtokoma ku madera onse a mfumu, kuti aononge ndi kupha Ayuda, ndipo afafaniziretu mtundu wonse wa Ayudawo. Aononge anyamata, anthu okalamba, azimai ndi ana omwe pa tsiku limodzi, pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara, ndipo afunkhe katundu wao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help