Mla. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zisangalatso nzopanda phindu

1Nthaŵi zina mumtima mwangamu ndinkati, “Ah! Tsopano ndiyesepo zokondweretsa, ndidzisangalatse.” Koma ai, zimenezinso zinali zopanda phindu.

2Kukakhala kuseka, ndidati, “Imene ija ndi misala.” Chikakhala chisangalatso, ndidati, “Phindu lake nchiyani?”

3Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.

4 1Maf. 10.23-27; 2Mbi. 9.22-27 Ndidaachita ntchito zazikulu. Ndidaamanga nyumba zambiri, ndi kudziwokera mipesa.

5Ndidaalima madimba ndi minda ya mitengo. Ndidaabzalamo mitengo yazipatso ya mitundu yonse.

6Ndidaakumbanso maiŵe oti madzi ake azithirira minda ya mitengo yobzala ija.

71Maf. 4.23 Ndidaagula akapolo ndi adzakazi, ndinalinso ndi akapolo obadwira m'nyumba mwanga momwe. Ndinali ndi ng'ombe ndi nkhosa kupambana aliyense amene adalamulirapo ku Yerusalemu kale.

81Maf. 10.10, 14-22 Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.

9 1Mbi. 29.25 Ndidaasanduka munthu wotchuka, nkudzapambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale, monsemo nzeru osandichoka.

10Chilichonse chimene maso anga ankachilakalaka, ndidaachitenga. Mtima wanga sindidaumane zokondweretsazo, pakuti mtima wangawo unkakondwa ndi ntchito zanga zonse zolemetsa. Zimenezi zinali mphotho ya ntchito zanga zolemetsazo.

11Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi.

12Pamenepo ndidayesanso kulingalira kuti kwenikweni nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Kodi munthu wodzaloŵa ufumu tsopanoyo angapose bwanji mnzake adapita uja? Nzokhazokhazo zomwe ameneyo adazichita kale.

13Ndidaona kuti inde nzeru nzopambana uchitsiru, monga momwe kuŵala kumapambanira mdima.

14Inde munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda m'chimbulimbuli. Komabe ndidazindikira kuti zomwe zagwera winayo, mnzakeyonso zimamgwera zomwezo.

15Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu!

16Pakuti munthu wanzeru, pamodzi ndi chitsiru chomwe, onsewo sakumbukika nthaŵi yaitali, pokhala kuti pa masiku akutsogolo, onsewo adzaiŵalika. M'mene chimafera chitsiru ndi m'menenso amafera munthu wanzeru.

17Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Kugwira ntchito nkungodzivuta chabe

18Ntchito zanga zonse zolemetsa zimene ndidazigwira pansi pano zidandiipira, chifukwa ndiyenera kuzisiyira amene adzabwere pambuyo panga.

19Tsono ndani amadziŵa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala womalamulira zonse zimene ndidazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Zimenezinso nzopanda phindu.

20Motero ndidayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndidazigwira movutikira pansi pano.

21Paja nthaŵi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri.

22Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhaŵa zimene amazichita pansi pano?

23Yob. 5.7; 14.1 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta. Ndi usiku womwe mtima wake supumula. Zimenezinso nzopanda phindu.

24 Mla. 3.13; 5.18; 9.7; Yes. 56.12; Lk. 12.19; 1Ako. 15.32 Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu.

25Nanga popanda Iye ndani angathe kudya, ndani angathe kusangalala?

26Yob. 32.8; Miy. 2.6 Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help