1 tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata.
20Motero anthu amalonda ogulitsa zinthu zamitundumitundu ankagona kunja kwa mzinda wa Yerusalemu kamodzi kapena kaŵiri konse.
21Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata.
22Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika.
23 Eks. 34.11-16; Deut. 7.1-5 Nthaŵi imeneyo ndidaona Ayuda amene adaakwatira akazi a ku Asidodi, a ku Amoni ndiponso a ku Mowabu.
24Mwakuti theka limodzi la ana ao ankalankhula chilankhulo cha ku Asidodi, sankathanso kulankhula Chiyuda, koma ankalankhula chilankhulo cha anthu a mitundu inayo.
25Tsono ndidakangana nawo ndi kuŵatemberera. Ndidamenya ena mwa iwo ndi kuŵazula tsitsi. Ndipo ndidaŵalumbiritsa m'dzina la Mulungu kuti, “Musadzakwatitse ana anu aakazi kwa amuna achilendo, ndipo ana anu aamuna ndi inu nomwe musakwatire akazi achilendo.
262Sam. 12.24, 25; 1Maf. 11.1-8 Kodi Solomoni mfumu ya Aisraele suja adachimwa chifukwa cha akazi otereŵa? Pakati pa mitundu ya pansi pano panalibe mfumu yofanafana naye. Mulungu ankamkonda ndipo adamuika kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Komabe akazi achilendo adachimwitsa ngakhale iyeyo.
27Monga tsopano tizimva kuti inunso mumachita choipa chachikulu chomwechi cha kuipira Mulungu pomakwatira akazi achilendo?”
28 Neh. 4.1 Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe uja, anali atakwatira mwana wa Sanibalati wa ku Horoni. Nchifukwa chake ndidampirikitsa kuti achoke ku Yerusalemu.
29Inu Mulungu wanga, mukumbukire m'mene anthuwo adaipitsira unsembe wao ndi m'mene adanyozera chipangano chimene mudachita ndi Alevi.
30Umu ndimo m'mene ndidaŵayeretsera anthu poŵachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndidakhazikitsa ntchito za ansembe ndi za Alevi, kuti aliyense adziŵe bwino ntchito yake.
31Chinanso, ndidalamula kuti nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha azipereke pa nthaŵi yoyenera.
Inu Mulungu wanga, mukumbukire zonsezi ndipo mundikomere mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.