1Mulungu mwa chifundo chake adatipatsa ntchitoyi, nchifukwa chake sititaya mtima.
2Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.
3Koma ngakhale Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbika, ngwophimbika kwa okhawo amene akutayika.
4Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka.
5Motero polalika sitidzilalika tokha, koma timalalika Yesu Khristu, kuti ndiye Ambuye. Ife ndife atumiki anu chabe chifukwa cha Yesuyo.
6Gen. 1.3 Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.
7Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai.
8Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
9Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
10Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu.
11Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa.
12Motero ife timaperekedwa ku imfa, koma chimenechi chimakupatsani moyo.
13 Mas. 116.10 Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.
14Pakuti tikudziŵa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso pake.
15Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu.
Za kulimbikira m'chikhulupiriro16Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
17Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
18Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.