1Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja.
2Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo.
3Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee.
4Pamenepo alonda aja adachita mantha nayamba kunjenjemera, nkungoti gwa ngati anthu akufa.
5Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu.
6Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.
7Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, ‘Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.’ Kumbukirani zimene ndakuuzanizi.”
8Apo azimaiwo adachoka kumandako msanga, ali ndi mantha komanso ndi chimwemwe chachikulu, nathamanga kukauza ophunzira ake aja.
9Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza.
10Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.”
Zimene alonda aja adakasimba11Pamene akazi aja ankapita, ena mwa alonda aja adakafika ku mzinda, nakasimbira akulu a ansembe zonse zimene zidaachitika.
12Tsono akulu a ansembe aja ndi akulu a Ayuda adasonkhana napangana nzeru. Adapatsa alonda aja ndalama zambiri,
13naŵauza kuti, “Muziti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku nkuba mtembo wake ife tili m'tulo.’
14Choncho bwanamkubwa akamva zimenezi, ife tidzamkhazika mtima pansi, ndipo sipadzakhala kanthu kokuvutani.”
15Alonda aja atalandira ndalama zija, adachitadi monga momwe adaaŵauzira. Motero mbiri imeneyi idawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.
Yesu atuma ophunzira ake(Mk. 16.14-18; Lk. 24.36-49; Yoh. 20.19-23; Ntc. 1.9-11)16 Mt. 26.32; Mk. 14.28 Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane.
17Pamene adamuwona, adampembedza, koma ena ankakayika.
18Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
19Ntc. 1.8Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
20Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.