Gen. 48 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe adalitsa Efuremu ndi Manase

1Patapita kanthaŵi, Yosefe adamva kuti “Bambo wanu akudwala.” Adatenga ana ake aŵiri, Manase ndi Efuremu, napita nawo kwa Yakobe.

2Yakobeyo atamva kuti “Mwana wanu Yosefe wabwera kudzakuzondani,” adadzilimbitsa, nadzuka, nkukhala tsonga pabedi pompo.

3Gen. 28.13, 14 Adauza Yosefe kuti, “Mulungu Mphambe amene adandiwonekera ku Luzi m'dziko la Kanani, adandidalitsa.

4Adandiwuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri kotero kuti zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako kuti likhale lao mpaka muyaya.’

5Tsono ana ako aŵiri, amene udabereka ku Ejipito kuno, ine ndisanabwere, amenewonso ndi anga. Efuremu ndi Manase adzakhala anga ndithu, monga momwe aliri Rubeni ndi Simeoni.

6Koma obadwa pambuyo pa iwowo, ndi ako amenewo. Adzalandira choloŵa chao pamodzi ndi achibale ao.

7Gen. 35.16-19Ndachita zimenezi chifukwa chakuti pamene ndinkabwerera kuchokera ku Mesopotamiya, mai wako Rakele adafera m'dziko la Kanani, mtunda wofika ku Efurata ukadalipo. Chisoni changa chinali chachikulu. Tsono ndidamuika komweko pa mseu wa ku Efurata ku Betelehemu.”

8Yakobe ataona ana a Yosefe, adafunsa kuti, “Nanga anyamata aŵa nga yani?”

9Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.”

10Maso a Yakobe sankapenya bwino chifukwa cha ukalamba. Yosefe adabwera nawo kwa iye anawo ndipo Yakobe adaŵakumbatira, naŵampsompsona.

11Yakobe adauza Yosefe kuti, “Sindinkayembekeza kuti ndingakuwonenso, koma tsopano Mulungu wandilola kuti ndiwone ndi ana ako omwe.”

12Tsono Yosefe adatenga anawo kuŵachotsa pa maondo a Yakobe. Ndipo adamgwadira.

13Yosefe adaŵagwira padzanja anawo, Efuremu ku dzanja lamanja kuti pakutero akhale ku dzanja lamanzere la Yakobe. Manase adakhala kumanzere kuti pakutero akhale ku dzanja lamanja la Yakobe.

14Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu.

15Ndipo adadalitsa Yosefe ndi mau akuti,

“Mulungu amene makolo anga

Abrahamu ndi Isaki adamtumikira,

Mulungu amene wanditsogolera

moyo wanga wonse mpaka lero lino,

aŵadalitse anaŵa!

16Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse,

aŵadalitsenso!

Podzera mwa anaŵa,

dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki

akhale omveka nthaŵi zonse!

Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa,

adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!”

17Yosefe ataona kuti bambo wake wasanjika dzanja lamanja pamutu pa Efuremu, adakhumudwa. Motero adatenga dzanja la bambo wake kulichotsa pamutu pa Efuremu, nalisanjika pamutu pa Manase.

18Adauza bambo wake kuti, “Musatero atate. Wamkulu ndi uyu. Dzanja lanu lamanja likhale pamutu pa ameneyu.”

19Koma bambo wakeyo adakana nati, “Ndikudziŵa, mwana wanga, ndikudziŵa. Adzukulu a Manase adzakhalanso anthu otchuka, koma mng'ono wakeyu adzatchuka kupambana iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yaikulu ya anthu.”

20Ahe. 11.21 Motero adaŵadalitsa pa tsiku limenelo ndi mau akuti,

“Aisraele adzatchula maina anu podalitsa.

Adzanena kuti,

‘Mulungu akudalitseni inu

monga Efuremu ndi Manase.’ ”

Mwa njira imeneyi adaika Efuremu patsogolo pa Manase.

21Pambuyo pake Yakobe adauza Yosefe kuti, “Ukuwonatu kuti ndili pafupi kufa, koma Mulungu adzakhala nawe, ndipo adzakubweza ku dziko la makolo ako.

22Ndiponso iweyo, osati abale ako, ndikukupatsa Sekemu, dera lija limene ndidachita cholanda ndi lupanga langa ndi uta wanga kwa Aamori.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help