Eks. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Dzombe

1Chauta adauza Mose kuti, “Upite kwa Farao. Ndamuumitsa mtima iyeyo ndi nduna zake, kuti ndichite zozizwitsa zonsezi pakati pao.

2Ndipo inu, mudzaŵauze ana anu ndi zidzukulu zanu za m'mene ndidapusitsira Aejipito, pamene ndinkachita zozizwitsa pakati pao. Motero nonsenu mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

3Mose ndi Aroni adapita kwa Farao kukamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Ahebri, akufunsa kuti, ‘Kodi udzakanabe kundigonjera mpaka liti? Uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.

4Ukakanabe kuŵalola kuti apite, ndikugwetsera dzombe maŵa m'dziko mwako.

5Nthaka yonse idzaphimbidwa ndi dzombelo, ndipo nthakayo sidzaoneka konse. Lidzadya zonse zomwe sizidaonongeke ndi matalala aja. Lidzadya mitengo yako yonse.

6Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja.

7Nduna za Farao zidafunsa Faraoyo kuti, “Kodi munthu ameneyu adzaleka liti kutivuta chotere? Aloleni anthuwo kuti apite, akapembedze Chauta, Mulungu wao. Kodi simukuwona kuti dziko la Ejipito latheratu kuwonongeka tsopano?”

8Motero Farao adaitananso Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta, Mulungu wanu. Koma tsono apite ndani?”

9Mose adayankha kuti, “Tidzapita tonse ndi ana athu, pamodzi ndi nkhalamba zathu zomwe. Tidzapita ndi ana aamuna, ana aakazi, nkhosa zathu ndi mbuzi zomwe. Tidzatenganso ndi ng'ombe zomwe, chifukwa choti tikachita mwambo wachipembedzo wolemekeza Chauta.”

10Choncho Farao adaŵauza kuti, “Chauta akhale nanu ngati ine ndikulolani kuti mutenge akazi anu ndi ana anu. Nchodziŵikiratu kuti inu mukufuna kudzetsa mavuto.

11Ai! Inu, amuna nokhanu, ndiye mupite mukapembedze Chauta, popeza kuti ndi zimene mukufuna.” Atangomveka mau ameneŵa, Mose ndi Aroni adapirikitsidwa pamaso pa Farao.

12Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Ejipito kuti dzombe libwere, ndipo lidzadye zomera zonse zimene matalala aja adasiya.”

13Choncho Mose adakweza ndodo yake kumwamba, ndipo Chauta adautsa mphepo yakuvuma kuti iwombe pa dziko usana ndi usiku womwe. Pamene kunkacha, nkuti ponseponse pali dzombe lokhalokha.

14Chiv. 9.2, 3 Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso.

15Lidangophimba nthaka yonse, ndipo nthakayo idada kuti bii chifukwa cha dzombelo. Lidadya kalikonse komera pa nthaka, pamodzi ndi zipatso zam'mitengo zimene matalala adasiyako. Palibe chachiŵisi chilichonse chimene chidatsalako pa mtengo kapena pa chomera chilichonse m'dziko lonse la Ejipito.

16Ndipo Farao adaitana Mose ndi Aroni mofulumira naŵauza kuti, “Ndachimwira Chauta, Mulungu wanu, ndipo ndachimwiranso inu.

17Koma pepani tsopano, khululukireni pa nthaŵi ino yokha, mupemphe kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti andichotsere chilango choopsachi.”

18Mose adachoka kwa Farao kuja, nakapemphera kwa Chauta.

19Chauta adasintha mphepoyo kuti ikhale mphepo yamkuntho yakuzambwe, ndipo idapirikitsira dzombelo ku Nyanja Yofiira. Palibe dzombe ndi limodzi lomwe limene lidatsalako ku Ejipito kuja.

20Koma Chauta adamuumitsabe mtima Farao, ndipo sadaŵalole Aisraele kuti apite.

Mdima

21 Lun. 17.1-21 Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti pagwe mdima wandiweyani pa dziko lonse la Ejipito.”

22Mas. 105.28; Chiv. 16.10 Mose adakweza dzanja lake kumwamba, ndipo pa masiku atatu, mudagwa mdima wandiweyani m'dziko lonse.

23Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku.

24Apo Farao adaitana Mose namuuza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta. Mupite nawonso akazi anu ndi ana anu omwe. Koma nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zomwe, zidzasungidwa konkuno.”

25Mose adati, “Tsonotu muyenera kutipatsa ndinu zokaperekera nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wathu.

26Koma iyai, zoŵeta zathu zidzapita nafe limodzi ndipo sipadzatsala choŵeta nchimodzi chomwe kuno. Tiyenera kukasankha zoŵeta zokapembedzera nazo Chauta, Mulungu wathu. Mpaka tikafike kumeneko, sitingadziŵe zoyenera kuzigwiritsa ntchito popembedza Chauta.”

27Koma Chauta adaumitsa Farao mtima, ndipo sadalole kuti anthuwo apite.

28Farao adauza Mose kuti, “Choka apa. Chenjera, ndipo usafikenso pamaso panga, chifukwa tsiku lomwe ndidzakuwonelo, udzaphedwa ndithu.”

29Mose adayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, ine sindidzakuwonaninso.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help