1 Mbi. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Lonjezo la Mulungu kwa Davide(2 Sam. 7.1-17)

1Davide atayamba kukhazikika m'nyumba yachifumu, tsiku lina adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.”

2Natani adauza Davide kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Mulungu ali nanu.”

3Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti,

4“Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Sudzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo.

5Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatsogolera Aisraele mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema.

6Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?”

7“Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja, kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele.

8Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.

9Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko, kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija,

10kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidagonjetsa adani ako onse. Kuonjezera pamenepo, ndikukuuza kuti Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako.

11Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako kumanda, Ine ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba.

12Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya.

132Ako. 6.18; Ahe. 1.5 Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo kuti uloŵe ufumu ndiwe.

14Koma ndidzamkhalitsa mu Nyumba yanga ndi mu ufumu wanga, ndipo ufumu wake udzakhala mpaka muyaya.’ ”

15Natani adalankhula ndi Davide potsata mau onseŵa, ndiponso potsata zimene adaaziwona m'masomphenyaŵa.

Pemphero la Davide lothokoza(2 Sam. 7.18-29)

16Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa?

17Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Mulungu. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandiwonetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Chauta Mulungu.

18Ndipo nchiyaninso chimene Davide anganene kwa Inu, popeza kuti mwamchitira ulemu chotere mtumiki wanu? Zoonadi Inu mumamdziŵa mtumiki wanu.

19Chifukwa chokonda mtumiki wanu, ndiponso malinga ndi mtima wanu, Inu Chauta, mwachita chinthu chachikulu choterechi, pondidziŵitsa zakutsogolozi.

20Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu Chauta, ndipo palibe mulungu wina koma Inu nokha.

21Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamene ankafika anthu anu, amene mudaŵaombola ku Ejipito.

22Inu mudaŵasandutsa anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anu mpaka muyaya, ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao.

23“Tsopano Inu Chauta, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa, muchite monga momwe mudaanenera.

24Choncho dzina lanu lidzakhala lomveka mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israele, ndiyedi Mulungu wao wa Israele!’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.

25Inu Mulungu mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pempheroli kwa Inu.

26Inu Chauta, ndinu Mulungu, ndipo mwalonjeza zinthu zabwino zimenezi kwa mtumiki wanu.

27Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pajatu zimene Inu Chauta mwazidalitsa, zimakhala zodalitsidwadi mpaka muyaya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help