1Dziko lakumwamba, imva zimene ndikuti ndilankhule.
Dziko lapansi imva mau a pakamwa panga.
2Zophunzitsa zanga zigwe ngati mvula,
mau anga atsike ngati mame,
ngati mvula yowaza pa msipu wanthete,
ngati mvula yamphamvu pa udzu watsopano.
3Ndidzatamanda dzina la Chauta.
Tamandani ukulu wake wa Mulungu.
4Chauta ndi Thanthwe,
ntchito zake ndi zangwiro,
njira zake zonse ndi zolungama,
ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse,
wachilungamo ndi wosalakwa.
5Koma inu ndinu osakhulupirika,
osayenera kukhala anthu ake,
ndinu mtundu wochimwa ndi wonyenga.
6Inu anthu opusa ndi opanda nzeru konse,
kodi mungamubwezere zotere Chauta?
Iye ndiye Atate anu ndi Mlengi wanu,
ndiye adakupangani ndi kukusandutsani mtundu.
7Kumbukirani zakale,
lingalirani zamakedzana ndithu,
funsani atate anu,
akuuzani zimene zidachitika.
Funsani akuluakulu,
akufotokozerani zakalezo.
8 Ntc. 17.26 Pamene Wopambanazonse adapereka maiko
kwa anthu a mitundu ina,
pamene adalekanitsa anthu,
adaŵaikira malire potsata kuchuluka
kwa anthu a Mulungu.
9Pajatu chigawo cha Chauta ndicho anthu ake,
zidzukulu za Yakobe ndizo chigawo chakechake.
10Adaŵapeza m'chipululu,
kuthengo kwenikweni kopanda kanthu.
Adaŵatchinjiriza, ndipo adaŵasamala,
monga momwe akadasamalira diso lake.
11Adachita ngati mphungu
imene ikuphunzitsa ana ake kuuluka,
imene ikungozungulira pamwamba pa ana akewo
nitambalitsa mapiko ake, kuti igwire anawo
ndi kuŵanyamula pa mapiko ake otambalitsa.
12Chauta yekha ndiye adatsogolera anthu ake,
popanda thandizo la milungu yachilendo.
13Adaŵathandiza kuti azilamula maiko amapiri,
ndipo adadya zomera zam'minda.
Adaŵadyetsa uchi wam'mathanthwe,
ndi mafuta ochokera m'nthaka yamiyala.
14Adaŵamwetsa chambiko wochokera ku ng'ombe
ndiponso mkaka wankhosa,
adaŵadyetsa nkhosa ndi mbuzi zonenepa,
ndiponso nkhosa zamphongo zabwino za ku Basani,
pamodzi ndi tirigu wabwino ndi vinyo wokoma.
15Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala,
koma iwowo adamuukira,
adanenepa ndi kukula thupi,
ndipo adakhuta zedi,
kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao,
nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao.
16Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo,
ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa.
17 1Ako. 10.20 Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa,
imene siili milungu konse,
milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse,
milungu yongobwera kumene,
milungu imene makolo ao sankailemekeza konse.
18Adakana mtetezi wao amene adaŵalenga,
adaiŵala Mulungu amene adaŵapatsa moyo.
19Chauta ataona zimenezi,
adaŵakana anthuwo,
chifukwa ana ao aamuna ndi aakazi
adaautsa mkwiyo wake.
20Iye adati, “Ndidzaŵafulatira,
ndidzaona chomwe chidzaŵachitikire,
chifukwa anthu ameneŵa ngonyenga,
ndi ana osakhulupirika.
21 1Ako. 10.22; Aro. 10.19 Milungu yao yabodza ndachita nayo nsanje,
mafano ao andikwiyitsa nawo.
Inenso ndidzaŵachititsa nsanje
pakusamalira mtundu wina wachabechabe,
ndipo ndidzaŵapsetsa mtima
pakukondera fuko lina lopanda pake.
22Mkwiyo wanga udzayaka ngati moto,
udzafika mpaka ku dziko la anthu akufa.
Udzatentha zonse pa dziko,
udzapsereza ndi mapiri omwe mpaka m'tsinde mwake.
23Ndidzaŵaunjikira masoka osatha,
mipaliro yanga yonse idzathera pa iwowo.
24Ndidzaŵatumizira njala yoopsa,
malungo ndi nthenda zofa nazo.
Ndidzaŵatumizira zilombo zakuthengo zoŵavuta,
zokwaŵa zaululu zidzaŵaluma.
25M'miseu adzafa chifukwa cha nkhondo,
m'nyumba adzafa ndi mantha.
Anyamata ndi atsikana adzafa,
ngakhale ana ndi okalamba omwe sadzakhala ndi moyo.
26Achikhala ndidangoŵaononga kotheratu onsewo,
kuti anthu pansi pano asaŵakumbukire ndi mmodzi yemwe!
27Koma sindifuna kuti adani ao azikandinyadira,
sindifuna kuti adani azikaganiza molakwa,
namanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwo ndife,
si Mulungu amene adachita zonsezi.’ ”
28Aisraele ndi mtundu wopanda maganizo,
alibe ndi nzeru zomwe.
29Achikhala anzeru, akadamvetsa,
ndipo akadazindikira zimene zitha kudzaŵagwera.
30Nanga chifukwa chiyani munthu mmodzi
adagonjetsa anthu chikwi chimodzi,
ndipo anthu aŵiri adagonjetsa zikwi khumi?
Nchifukwa chakuti Chauta, Mulungu wao, waŵasiya,
Mulungu wao wamphamvu waŵataya.
31Adani ao amadziŵa
kuti milungu yao ndi yopanda mphamvu,
ndi yosalingana ndi Mulungu wa Aisraele.
32Adani ao ndi oipitsitsa ngati Sodomu ndi Gomora,
Ali ngati mipesa yobala mphesa zoŵaŵa ndi zaululu,
33ndi oipa kwambiri
ngati vinyo wosanganiza ndi ululu wa njoka,
ululu wopweteka wa mphiri.
34Zimenezitu ndazisunga,
ndi zobisika m'chikatikati cha mumtima mwanga.
35 Aro. 12.19; Ahe. 10.30 Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso,
nthaŵi yoti agwe idzakwana.
Tsiku la masoka ao layandikira,
chiwonongeko chao chikudza mofulumira.
36 Mas. 135.14 Chauta adzachitira anthu ake zolungama,
adzachitira atumiki ake zachifundo,
pamene adzaona kuti mphamvu zao zatha,
ndipo kuti sipatsala anthu,
kaya ndi akapolo kapena mfulu.
37Pamenepo Chauta adzafunsa anthu ake kuti,
“Nanga milungu yamphamvu yomwe mumaikhulupirira ija
ili kuti?
38Mudaidyetsa mafuta a nsembe zanu,
mudaipatsa vinyo woti imwe.
Ibweretu kuti ikuthandizeni, ikutetezeni.
39Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine,
Ine ndekha, palibenso mulungu wina.
Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo,
ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe
amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga.
40Ndikukweza dzanja kumwamba,
ndikulumbira pali Ine ndemwe wa moyo wosatha,
41kuti ndidzanola lupanga langa lochezimira,
ndipo ndidzaona kuti chilungamo chichitike.
Adani anga ndidzaŵabwezera chilango,
amene amadana nane ndidzaŵalanga.
42Mivi yanga idzafiira ndi magazi ao
ndipo lupanga langa lidzabayadi mnofu wao.
Olasidwa ndi ogwidwa ukapolo magazi ao adzafalikadi,
ndiponso mitu yao ya tsitsi litalilitali idzadulidwa.”
43 Aro. 15.10; Chiv. 19.2 Inu mitundu yonse ya anthu,
tamandani anthu a Chauta.
Chauta amalanga onse opha anthu ake,
amalipsira adani ake,
ndipo amachotsa tchimo m'dziko la anthu ake.
44Mose ndi Yoswa mwana wa Nuni adanena pamtima mau onse a nyimbo imeneyi, ndipo Aisraele ankamva.
Malangizo otsiriza a Mose45Mose atatha kuphunzitsa anthu mau onseŵa,
46adati: Mukumbukire bwino malamulo onse amene ndakupatsani leroŵa. Muuze ana anu kuti azimvera mosamala mau onse a malamuloŵa.
47Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani.
48 Num. 27.12-14; Deut. 3.23-27 Tsiku lomwelo, Chauta adalankhula ndi Mose kuti,
49“Kwera phiri loti Nebo ku mtandadza wa mapiri a Abarimu, umene uli m'dziko la Mowabu, kuyang'anana ndi mzinda wa Yeriko. Ulipenye dziko la Kanani limene ndikuŵapatsa Aisraele.
50Iwe udzafera pa phiri limenelo, monga mbale wako Aroni adafera pa phiri la Horo.
51Chifukwa chake nchakuti inu nonse aŵiri simudakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraele. Pamene munali ku madzi a Meriba, pafupi ndi mudzi wa Kadesi, m'chipululu cha Zini, simudandilemekeze kokwanira pamaso pa Aisraele.
52Nchifukwa chake dziko limene ndikupatsa Aisraele uliwonere chapatali, koma kuloŵa kokha ndiye ai, suloŵamo”.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.