1 2Maf. 23.36—24.6; 2Mbi. 36.5-7 Pa nthaŵi imene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya, anali mfumu ya ku Yuda, Chauta adalankhula nane ine Yeremiya. Adati,
2“Pita ku banja la Arekabu, ukaŵaitane anthu akumeneko kuti abwere m'chipinda chimodzi cha Nyumba ya Chauta. Atafika, uŵapatse vinyo kuti amwe.”
3Motero ndidabwera ndi Yazaniya (mwana wa Yeremiya winanso, mwana wa Habaziniya,) pamodzi ndi abale ake ndiponso ana ake onse aamuna, ndiye kuti banja lonse la Arekabu.
4Ndidabwera nawo ku nyumba ya Chauta, ku chipinda cha ophunzira a Hanani, mwana wa Igadaliya, munthu womvera Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, pamwamba pa chipinda cha Maseiya, mwana wa Salumu, mlonda wapakhomo.
5Tsono ndidaika mbiya zodzaza ndi vinyo ndi zikho zomwera pamaso pa Arekabuwo, ndipo ndidaŵauza kuti, “Nayu vinyo, imwani.”
6Koma iwowo adati, “Ife sitimwa vinyoyu, poti kholo lathu Yonadabu mwana wa Rekabu adatilamula kuti, ‘Musadzamwe vinyo, inuyo ndi ana anu omwe.
7Musadzamange nyumba kapena kubzala mbeu, kapena kulima minda yamphesa. Zinthu zimenezi musadzakhale nazo. M'malo mwake muzidzangokhala m'mahema pa moyo wanu wonse, kuti mukhale nthaŵi yaikulu m'dziko limene mukukhalamo.’
8Takhala tikutsata malamulo a kholo lathu Yonadabu, mwana wa Rekabu, ndipo pa moyo wathu wonse sitidamwe vinyo ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi.
9Sitidamange nyumba kuti tizikhalamo, kapena kulima minda yamphesa kapena minda ina iliyonse.
10Tangokhala m'mahema basi. Motero tamvera ndi kusunga malamulo onse a kholo lathu Yonadabu.
11Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adathira nkhondo dziko lino, tidanena kuti, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithaŵe magulu ankhondo a Ababiloni ndi a Asiriya.’ Nchifukwa chake tikukhala kuno ku Yerusalemu.”
12Tsono mau a Chauta adadza kwa Yeremiya onena kuti,
13Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akuti, “Pita ukafunse anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko nzeru ndi kumvera mau anga?’
14Lamulo la Yonadabu, mwana wa Rekabu, limene adalamula zidzukulu zake kuti asadzamwe vinyo, iwowo asungadi. Samwa vinyo mpaka lero lino chifukwa chomvera lamulo la kholo lao. Ndakhala ndikulankhula nanu kaŵirikaŵiri kukuchenjezani, komabe simudandimvere.
15Ndidatuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Aliyense mwa inu asiye ntchito zake zoipa. Konzani makhalidwe anu, ndipo muleke kutsata milungu ina, musamaipembedza. Motero mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu.’ Komabe inu simudalabadeko, simudandimvere.
16Ana a Yonadabu, mwana wa Rekabu, adatsata lamulo limene kholo lao lidaŵapatsa. Koma inuyo simudandimvere ai.
17Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndikuti ndidzaŵaononga Ayuda ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu, chifukwa chakuti sadandimvere pamene ndidaŵalankhula, sadandiyankhe nditaŵaitana.”
18Yeremiya adauza Arekabu aja mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Chifukwa chakuti mudamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndipo mudatsata malangizo ake ndi kuchita zonse zimene adakuuzani kuti muchite,
19tsono Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasoŵa mdzukulu wonditumikira mpaka muyaya.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.