1 1Am. 7.49; 2Am. 15.36 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara, pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, pamene lamulo loyamba lija la mfumu lidaayenera kulitsata, limene adani a Ayuda ankayembekeza kuŵaononga, zinthu zidasinthika. Ayuda ndiwo adayamba kuwononga adani ao tsiku lomwelo.
2Ayudawo adasonkhana m'mizinda yao, m'madera onse a mfumu Ahasuwero, kuti aononge munthu aliyense amene ankafuna kuŵachita choipa. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene akadatha kulimbana nawo, poti anthu a mitundu yonse ankaŵaopa kwambiri Ayudawo.
3Akuluakulu onse a m'madera amenewo, akalonga, akazembe ndi atsogoleri a boma, onsewo ankathandiza Ayuda chifukwa choti ankamuwopa kwambiri Mordekai.
4Pajatu anali munthu wamkulu wa ku nyumba ya mfumu ndipo mbiri yake idaawanda ponseponse m'madera onse, chifukwa ulamuliro wake unkapita nukulirakulira mphamvu.
5Motero Ayuda adapha adani ao onse ndi lupanga. Adaŵapha ndi kuŵaononga, nachita nawo monga momwe ankafunira.
6Mu mzinda wa Susa, likulu la dziko, Ayuda adapha ndi kuwononga anthu okwanira mazana asanu.
7Adaphanso Parasadata, Dalifoni, Asipata,
8Porata, Adaliya, Aridata,
9Parisita, Arisai, Aridai, Vaizata,
10ndi ana aamuna khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sadafunkhe zinthu zao.
11Tsiku lomwelo chiŵerengero cha anthu ophedwa mu mzinda wa Susa, likulu la dziko, adachitumiza kwa mfumu.
12Ndipo mfumu idamuuza Estere kuti, “Mu mzinda waukulu wokha uja wa Susa, Ayuda apha anthu mazana asanu, kuphatikizapo ana aamuna khumi a Hamani. Nanga nanji tsono m'madera ena onse a mfumu, afikitsa angati? Tsono ukupemphanso chiyani? Chopempha chakocho ndidzakupatsa. Nanga nchiyaninso chimene ukuchifunabe? Chimene ukuchifunacho ndidzakupatsa.”
13Apo Estere adauza mfumuyo kuti, “Chikakukomerani inu amfumu, mulole kuti Ayuda okhala mu mzinda wa Susa aloledwe maŵa kuti achitenso zimene achita lerozi potsata lamulo. Ndipo ana aamuna khumi a Hamani aja mitembo yao ipachikidwe pa mtengo.”
14Choncho mfumu idalamula kuti zimenezi zichitikedi. Lamulo lidaperekedwa mu mzinda wa Susa, ndipo mitembo ya ana aamuna khumi a Hamani aja adaipachika pa mtengo.
15Pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara, Ayuda okhala ku Susa adasonkhananso pamodzi, ndipo adapha anthu enanso okwanira mazana atatu ku Susako. Koma sadafunkhe zinthu zao.
16Nawonso Ayuda okhala m'madera a mfumu adasonkhana kuti ateteze moyo wao, ndipo adaononganso adani ao aja. Adapha anthu amene ankadana nawo okwanira 75,000. Koma sadafunkhe zinthu zao.
17Zimenezi zidachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara. Pa tsiku la 14 adapumula, ndipo adalisandutsa tsiku la madyerero ndi lachikondwerero.
18Koma Ayuda okhala ku Susa amene adaasonkhana pa tsiku la 13 ndi pa tsiku la 14, adapumula pa tsiku la 15 nalisandutsa tsiku la madyerero ndi lachikondwerero.
19Nchifukwa chake Ayuda akumiraga, okhala m'mizinda yopanda malinga, amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati tsiku lachikondwerero, la madyerero ndi lopumula, losagwira ntchito. Ndipo pa tsiku limeneli amatumizirana mphatso.
20Pambuyo pake Mordekai adalemba zimenezi m'buku, natumiza makalata kwa Ayuda onse okhala ku madera onse a mfumu Ahasuwero, kufupi ndi kutali komwe.
21Adaŵauza kuti azisunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndi tsiku la 15 la mwezi womwewo chaka ndi chaka,
22popeza kuti masiku amenewo Ayuda adaapulumuka kwa adani ao, ndiponso mwezi umenewo chisoni chao chidaasanduka chimwemwe, kulira kwao kudaasanduka kukondwa. Adaŵauzanso kuti masiku amenewo azichita madyerero ndi kumasangalala potumizirana zakudya zabwino, ndiponso pomapatsa mphatso anthu osauka.
23Motero Ayuda adayamba kuchita zimene Mordekai adaŵalangiza m'kalata kuti azichita chaka ndi chaka.
24Esr. 3.7Hamani, Mwagagi uja, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda onse, anali atachita chiwembu choti aononge Ayuda, ndipo adaaombeza ula wa Puri, ndiye kuti maere, kuti aononge Ayudawo ndi kuŵafafaniziratu.
25Koma pamene Estere adadza pamaso pa mfumu, mfumu idalamula mochita kulemba ndithu kuti chiwembu cha Hamani chimene adaati aŵachite Ayuda, chigwere iyeyo, ndipo kuti iyeyo pamodzi ndi ana ake aamuna apachikidwe pa mtengo.
26Nchifukwa chake masiku ameneŵa amaŵatcha kuti masiku a Purimu potsata dzina loti Puri. Choncho chifukwa cha zonse zimene zidaalembedwa m'kalata imeneyi, ndipo chifukwa cha zimene adaakumana nazo pa nkhani imeneyi, ndiponso chifukwa cha zimene zidaaŵagwera,
27Ayudawo adadzipangira lamulo lokhalira iwowo. Lamulolo adapangira zidzukulu zao, ndi onse amene ankaphatikana nawo, kuti onsewo asamalephera kusunga masiku aŵiri ameneŵa, potsata zimene zidalembedwa ndiponso nthaŵi yake yochita zimenezi chaka ndi chaka.
28Masiku ameneŵa aziŵakumbukira ndi kumaŵasunga pa mibadwo yonse, m'banja lililonse, m'dziko lililonse ndiponso mu mzinda uliwonse. Masiku ameneŵa, otchedwa Purimu, asamaipitsidwa pakati pa Ayuda, ndipo zidzukulu zisadzaleke kuŵakumbukira.
29Tsono mfumukazi Estere, mwana wa Abihaili, ndiponso Myuda uja Mordekai, adapereka ulamuliro wonse wolembedwa, kuti atsimikizire kalata yachiŵiriyi yonena za Purimu.
30Makalata adatumizidwa kwa Ayuda onse ku madera onse aja 127 a mfumu Ahasuwero. Makalatawo anali onena za mtendere ndi za kukhulupirika,
31kuti masiku aŵa a Purimu aziŵasunga pa nyengo yake, potsata zimene Myuda Mordekai ndi mfumukazi Estere adalamula Ayuda. Aziŵasunga potsatanso malamulo amene adadziikira iwowo ndi zidzukulu zao, onena za kusala zakudya kwao ndi kulira kwao.
32Lamulo la mfumukazi Estere ndilo lidakhazikitsa Purimuyo, ndipo lidalembedwa m'buku.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.