1Naŵa malamulo ndi malangizo onse amene mudzayenera kuŵamvera nthaŵi zonse mudzakhale m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani.
2Mutalanda maiko a anthuwo, musadzalephere kuwononga kwathunthu malo onse amene iwo amapembedzerapo milungu yao, monga pa mapiri aatali ndi pa mapiri aafupi, ndiponso pansi pa mitengo yogudira.
3Deut. 7.5 Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse.
4Musakapembedze Chauta, Mulungu wanu, monga m'mene amachitira anthu ameneŵa popembedza milungu yao.
5Mulungu adzasankha malo amodzi m'dziko mwanu, ndipo anthu onse azidzabwera kudzampembedza pa malo amenewo. Kumeneko ndiko kumene mudzapite.
6Muzikapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zanu zina, zopereka zanu zachikhumi, ndi zopereka za mtundu wina, ndiponso mphatso zimene mumalonjeza kupereka kwa Mulungu, zopereka zanu zaufulu, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina.
7Kumenekonso inu pamodzi ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha madalitso amene Iyeyo adatsitsa pa inu, kuti ntchito zanu zonse ziyende bwino.
8Nthaŵi imeneyo ikadzafika, musadzachite m'mene timachitira kunomu. Mpaka tsopano lino, aliyense mwa inu amangopembedza monga akufunira,
9poti simunaloŵebe m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, kumene mudzatha kukhala mwamtendere.
10Mukaoloka mtsinje wa Yordani, Chauta, Mulungu wanu, adzakulolani kukakhala m'dziko limene Chauta adzakupatsani ngati choloŵa chanu. Adzakutchinjirizani kwa adani anu onse, kuti mukhale mwamtendere.
11Pamenepo Chauta adzasankhula malo oti anthu azidzapembedzerako, ndipo inu muzidzabwera kumeneko ndi zonse zimene ndakulamulanizi, monga nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zinanso, zopereka zanu zachikhumi ndi zopereka zanu zina, ndiponso mphatso zanu zapadera zimene mumalonjeza kwa Chauta.
12Tsono mudzakondwa pamaso pake inuyo, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi aakazi, pamodzi ndi Alevi amene ali m'midzi mwanu, poti paja iwo sadzalandira dziko laolao.
13Musadzapereke nsembe zopsereza pamalo paliponse.
14Muzikapereka nsembezo pa malo amodzi okha, amene Chauta adzasankhule pakati pa mafuko anu. Muzikapereka nsembe zanu zopsereza pa malo okhawo, ndipo kumenekonso muzikachita zina zonse zimene ndikukulamulani.
15Ku midzi yonse kumene mukakhale, mungathe kumakaphako zoŵeta zanu kuti muzikadya. Muzidzadya monga mungafunire, malinga nchifundo cha Chauta, Mulungu wanu, chimene Iye wakupatsani. Nonsenu muzikadya, amene ali oipitsidwa pa zachipembedzo ndi amene ali osaipitsidwa. Monga momwe mukadadyera nyama yamphoyo kapena yangondo, muzikachita chimodzimodzi.
16Gen. 9.4; Lev. 7.26, 27; 17.10-14; 19.26; Deut. 15.23 Magazi okha a nyamazo musadzadye, koma muzikaŵataya pansi ngati madzi.
17Ku midzi yonse kumene mukakhale, musadzadye chachikhumi cha tirigu wanu, kapena cha vinyo wanu kapena cha mafuta anu aolivi. Kumenekonso musakadye kalikonse kamene mwakapereka kwa Chauta, monga ana a ng'ombe ndi a zoŵeta zina oyamba kubadwa, kapena mphatso zimene mwalonjeza kuti mudzapereka kwa Chauta, kapena zopereka zanu zaufulu, kapena zopereka zina zilizonse.
18Inuyo ndi ana anu, pamodzi ndi antchito anu, ndi Alevi amene akhala m'midzi mwanu, muzikadya zopereka zonsezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atasankha. Kumenekonso muzidzasangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha ntchito zanu zonse zoyenda bwino.
19Muchenjere kuti, nthaŵi zonse mudzakhale m'dzikomo, musadzaiŵale Alevi.
20Chauta, Mulungu wanu, akadzalikuza dziko lanulo monga momwe adakulonjezerani, pamene mudzamva nkhuli, mudzatha kukhuta nyama monga momwe mudzafunire.
21Ngati ali patali malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankha kuti anthu azilemekezerako dzina lake, mungathe kupha ng'ombe yanu iliyonse kapena choŵeta china, monga ndidakuuzirani. Muphe nyama mwa zimene Chauta akupatsani, ndipo mudye nyama kwanu, monga momwe mungafunire.
22Aliyense woipitsidwa pa zachipembedzo kapena wosaipitsidwa adyeko nyamayo, monga momwe akadadyera nyama yamphoyo kapena yangondo.
23Lev. 17.10-14 Magazi okha musadye podya nyamayo, chifukwa moyo uli m'magazimo, motero inu musadye moyowo pamodzi ndi nyamayo.
24Magaziwo musadye, koma muŵataye pansi ngati madzi.
25Mukapanda kudya magaziwo, zonse zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, chifukwa cha kuchita zabwino motere pamaso pa Chauta.
26Zopereka zanu zimene mudapatulira Chauta pamodzi ndi mphatso zanu zimene mudalonjeza, zonsezo mupite nazo kwa Chauta pa malo achipembedzo amene adzaŵasankha.
27Kumeneko mukapereke nsembe zopsereza, nyama ndi magazi omwe, pa guwa la Chauta. Magazi ake mukathire pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, koma nyama yake mungathe kudya.
28Musamale zonse zimene ndakulamulanizi, ndipo mumvere mokhulupirika. Muchite zabwino zokhazokha zokondweretsa Chauta, Mulungu wanu, kuti zonse zidzakuyendereni bwino, inu ndi zidzukulu zanu.
Chenjezo kwa opembedza mafano29Chauta, Mulungu wanu, akadzaononga mitundu ina imene mudzalanda dziko lao, inu mudzakhala ndi kukhazikika m'dzikomo.
30Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?”
31Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.
32Deut. 4.2; Chiv. 22.18, 19 Musamale bwino kuti muchite zonse zimene ndakulamulani. Musaonjezepo kapena kuchotsapo kanthu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.