1Tsoka kwa inu amene mumakhala mosatekeseka ku Ziyoni,
ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya.
Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Aisraele,
inu amene anthu onse amafika kwanu.
2Pitani ku mzinda wa Kaline mukaone.
Mupitenso ku Hamati mzinda wotchuka uja,
tsono mutsikire ku Gati kwa Afilisti.
Kodi Aisraelenu mukupambana anthu a mafumu ameneŵa?
Kodi kapena dziko lao nlalikulu kupambana lanu?
3Inu simulabadako zoti kudzafika tsiku lachilango,
zochita zanu zimafulumizitsa nthaŵi yachiwawayo.
4Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi
oŵakongoletsa ndi minyanga yanjovu,
inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu,
nkumachita phwando la nyama ya anaankhosa
osakhwima ndi ya anaang'ombe onenepa.
5Ntchito nkumangoimba azeze ngati Davide,
ndi kumangopeka nyimbo
zoimbira pa zing'wenyeng'wenye.
6Tsoka kwa inu amene mumamwera vinyo
m'zipanda zodzaza,
inu amene mumadzola mafuta abwino kwambiri,
koma simumva chisoni ndi kuwonongeka
kwa dziko la Yosefe.
7Nchifukwa chake mudzatsogola ndinu
kupita ku ukapolo,
ndipo maphwando ndi zikondwerero zidzakutherani.
8Ambuye Chauta alumbira m'dzina lao kuti,
“Ndikunyansidwa ndi zimene ana a Yakobe akunyadira,
ndikudana nazo nyumba zao zazikulu.
Ndithu ndidzapereka kwa adani ao
likulu lao ndi zonse zam'menemo.”
9Anthu khumi akadzakhala akubisala m'nyumba imodzi, nawonso adzafabe.
10Mbale wake wa wina mwa akufawo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mtembo m'nyumbamo. Tsono adzafunsa wina amene watsalakobe m'nyumbamo kuti, “Kodi uli ndi winanso wamoyo m'menemo?” Iyeyo adzayankha kuti, “Ai mulibiretu.” Ndipo mbaleyo adzati, “Khala chete, iwe! Tisayerekeze kutchula dzina la Chauta.”
11Zoonadi, Chauta akadzangolamula,
nyumba zikuluzikulu zidzagamukagamuka,
ndipo nyumba zing'onozing'ono
ndiye zidzangosanduka zibuma zokhazokha.
12Kodi pa thanthwe akavalo nkuthamangapo?
Kodi panyanja wina nkulimapo ndi ng'ombe?
Komabe chilungamo mwachisandutsa chivumulo,
ndipo zaungwiro mwazisandutsa zoŵaŵa.
13Mukunyadira kuti mudagonjetsa mzinda wa Lodebara,
mukunena kuti, “Kodi suja tidapambana
mzinda wa Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
14Koma Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse akuti,
“Ndidzakuputirani anthu a mtundu wina
kuti adzakuthireni nkhondo, inu Aisraele.
Adzakuzunzani kuyambira ku Mpata wa Hamati kumpoto
mpaka ku mfuleni wa Araba kumwera.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.