Gen. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuchimwa kwa anthu a ku Sodomu

1Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati,

2“Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.”

3Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya.

4Alendowo asanakagone, anthu onse amumzindamo, achinyamata ndi okalamba omwe, adadzazinga nyumbayo.

5Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora

23Pamene dzuŵa linkatuluka, Loti nkuti atafika kale ku Zowari.

24Mt. 10.15; 11.23, 24; Lk. 10.12; 17.29; 2Pet. 2.6; Yuda 1.7 Tsono Chauta adagwetsa moto wa sulufule pa Sodomu ndi Gomora kuchokera kumwamba.

25Motero adaonongeratu mizinda imeneyi, pamodzi ndi chigwa chonse ndi anthu onse am'mizindamo, kuphatikizapo zomera zonse za m'dziko limenelo.

26Lun. 10.7; Lk. 17.32 Koma mkazi wa Loti adaacheukira m'mbuyo, ndiye pomwepo adasanduka mwala wamchere.

27M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adathamangira ku malo omwe aja, kumene adaaimirira pamaso pa Chauta.

28Adayang'ana ku mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi ku chigwa chija. Ndipo adangoona utsi uli tolotolo kutuluka m'chigwamo ngati utsi wotuluka m'ng'anjo ya moto.

29Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala.

Chiyambi chake cha Amowabu ndi Aamori

30Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga.

31Mwana wamkulu adauza mng'ono wake kuti, “Bambo athuŵa akukalamba tsopano, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe pa dziko lapansi woti angatikwatire, kuti tibale ana monga momwe zimachitikira zinthu pa dziko lapansi.

32Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe.

33Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.”

34M'maŵa mwake mwana wamkuluyo adauza mng'ono wake uja kuti, “Ine dzulo ndidagona ndi atate. Tiye tsono tiŵaledzeretsenso kuti iwenso ugone nawo, kuti choncho mtundu wathu usathe.”

35Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo.

36Mwa njira imeneyi, ana onse aŵiriwo a Loti adatenga pathupi pa bambo wao.

37Mwana wamkuluyo adabala mwana wamwamuna, namutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse.

38Mwana wamng'onoyo nayenso adabala mwana wamwamuna, namutcha Benami. Iyeyo ndiye kholo la Aamoni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help