Deut. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu oyenera kuchotsedwa mu msonkhano wa Chauta

1Mwamuna aliyense wofulidwa, kapena woduka chiwalo chaumuna, asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta.

2Mwana wam'chigololo asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta, ngakhale zidzukulu zake mpaka mbadwo wachikhumi.

3Neh. 13.1, 2 Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe msonkhano wa anthu a Chauta. Ngakhale mdzukulu wao aliyense mpaka mbadwo wachikhumi, asaloledwe kuloŵa mu msonkhano wa anthu a Chauta.

4Num. 22.1-6 Iwoŵa sadakupatseniko chakudya kapena madzi pa ulendo wanu uja wochoka ku Ejipito. Ndipo adalemba ntchito Balamu, mwana wa Beori, wa m'mudzi mwa Petori ku Mesopotamiya, kuti akutemberereni.

5Num. 23.7—24.9 Koma Chauta, Mulungu wanu, sadamumvere Balamuyo. Matembererowo adaŵasandutsa madalitso pa inu, popeza kuti adakukondani inu.

6Pa masiku onse a moyo wanu musachite kanthu kalikonse kothandiza anthu a mitundu imeneyi, kuti apeze mtendere kapena ubwino.

7Musaŵanyoze Aedomu. Amene aja ndi abale anu. Musaŵanyoze Aejipito, popeza kuti kale mudaakhala m'dziko mwao.

8Kuyambira pa mbadwo wachitatu mpaka muyaya, zidzukulu zao zingathe kuloŵa nao mu msonkhano wa anthu a Chauta.

Za kasamalidwe ka zithando zankhondo

9Mukakhala m'zithando pa nthaŵi yankhondo, muzilewa zonse zimene zingathe kukulakwitsani.

10Ngati mwamana aliyense pakati panu waipitsidwa chifukwa chakuti wadzilotera usiku, atuluke m'zithando ndipo akhale kunja kwa zithandozo.

11Madzulo asambe ndithu, ndipo pomaloŵa dzuŵa, abwerere ku zithando.

12Kunja kwa zithando, mukonze malo kumene mungathe kumapitako kukadzithandiza.

13Mwa zida zanu muzitenga chokumbira, kuti muthe kukumba kadzenje komadzithandizirapo, tsono mutatha, mufotsere.

14Zithando zanuzo zizikhala zaukhondo, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amayenda pakati pa zithando zanu, kuti akutchinjirizeni ndi kukupambanitsani kwa adani anu. Choncho m'zithando zanu mukhale mwabwino, kuti Chauta asaone kanthu kalikonse konyansa ndi kukufulatirani.

Malamulo osiyanasiyana

15Kapolo akathaŵa kwa mbuye wake, nkubwera kwa inu kuti mumsunge, musambweze kwa mbuyakeyo.

16Angathe kukhala pakati pa inu mu mzinda wanu uliwonse umene angasankhe ndiponso kumene kungamkomere, musamvute ai.

17 Lev. 19.29 Pakati pa ana a Aisraele pasakhale akazi kapena amuna okhala mahule a ku Nyumba ya Mulungu.

18Ndalama zozipeza mwa njira yadama yotereyi, yochitika ndi mkazi kapena mwamuna, musabwere nazo ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, kuti mukwaniritsire malonjezo anu, poti zimenezi Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo.

19 Eks. 22.25; Lev. 25.36, 37; Deut. 15.7-11 Mukakongoza mbale wanu ndalama, kapena chakudya kapena kanthu kena kalikonse, musamulipitse chiwongoladzanja pobweza.

20Mlendo yekha mungathe kumlipitsa chiwongoladzanja, koma osati mbale wanu. Lamulo limeneli mulimvere ndithu, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzadalitsa ntchito zanu zonse m'dziko limene mukukakhalamolo.

21 Num. 30.1-16; Mt. 5.33 Ukachita lonjezo kwa Chauta, Mulungu wako, usazengereze kuchita chimene walonjezacho. Chauta adzakuumiriza kuti uchichite, ndipo kuzengereza nkuchimwa.

22Koma ngati simulonjeza, apo palibe kulakwa ai.

23Choncho muzisunga mau amene adatuluka m'kamwa mwanu, chifukwa mudalonjeza mwaufulu kwa Chauta kuti mudzachitadi zimene mudalonjeza.

24Mukamayenda m'njira yodzera m'munda wamphesa wa mnzanu wokhala naye pafupi, mungathe kudyako mphesa zimene mungafune, koma musatengereko m'dengu pochoka.

25Mukayenda m'njira yodzera m'munda watirigu, mungathe kudyako ngala za tirigu mobudula ndi manja, koma musadule tirigu ndi chikwakwa m'munda mwa mnzanuyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help