1 Num. 21.4 Tidabwerera kupita ku chipululu podzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga momwe Chauta adatilamulira. Ndipo tidakhala tikuzungulira phiri la Seiri masiku ambiri.
2Tsono Chauta adandiwuza kuti,
3“Mwakhala mukuyenda uku ndi uku mozungulira dziko lamapirili nthaŵi yokwanira, tsopano tembenukani, mupite kumpoto.
4Gen. 36.8 Mulangize anthu kuti: Muli pafupi kubzola dziko la achibale anu, zidzukulu za Esau, amene akukhala m'Seiri. Iwowo adzakuwopani inu, koma inu muchenjere,
5musaŵapute, popeza kuti sindidzakupatsani dziko laolo, ngakhale mpoti muponde pomwe. Phiri la Seiri ndalipereka kwa zidzukulu za Esau.
6Chakudya mudzachita chogula ndi ndalama, madzi akumwanso mudzachita ogula ndi ndalama.”
7Chauta, Mulungu wanu, wakudalitsani pa ntchito zonse zimene mwachita. Wakusamalirani pa ulendo wanu m'chipululu chachikuluchi. Chauta, Mulungu wanu, wakhala nanu pa zaka makumi anai zonsezi, ndipo simudasoŵe kanthu kalikonse.
8Tsono tidapitirira ulendo wathu molambalala dziko la Seiri kumene kunali zidzukulu za Esau, ndipo tidasiya njira ya Araba yochokera ku mizinda ya Elate ndi Eziyoni-Gebere. Choncho tidatembenuka ndi kulunjika ku chipululu cha Mowabu.
9 Gen. 19.37 Ndipo Chauta adandiwuza kuti, “Musaŵavute Amowabu, zidzukulu za Loti. Musachite nawo nkhondo. Iwoŵa ndaŵapatsa dziko la Ari, ndipo sindikupatsani ngakhale gawo lomwe la dziko laolo.”
10(Kale ku Ari kunkakhala mtundu wina wa anthu otchedwa Aemimu. Anthu ake anali otchuka ndiponso ambiri. Kutalika kwao ankalingana ndi mtundu wina wa anthu otchedwa Aanaki.
11Monga Aanaki omwe, anthuwo ankadziŵika ndi dzina lakuti Arefaimu. Koma Amowabu ankaŵatchula kuti Aemimu.
12Ahorinso ankakhala ku Seiri, koma zidzukulu za Esau zidaŵapirikitsa, ndi kuwononga mtundu wonse. Atatero, iwo adakhala ku dziko la Seiri. Adachita zimenezi monga momwe Aisraele adapirikitsira adani ao m'dziko limene Chauta adaŵapatsa.)
13Tsono Chauta adaonjeza kuti, “Tsopano nyamukani, muwoloke mtsinje wa Zeredi.” Choncho tidaoloka mtsinje wa Zeredi.
14Num. 14.28-35 Nthaŵi imene tidaoloka mtsinje wa Zerediwo, nkuti patapita kale zaka 38 kuyambira pamene tidakhala ku Kadesi-Baranea. Amuna odziŵa kumenya nkhondo nkuti atafa onse, monga momwe adaanenera Chauta molumbira.
15Zoonadi dzanja la Chauta lidaŵakantha mpaka onse am'mahemawo adatha nkuwonongeka.
16Amuna onse omenya nkhondo atafa,
17Chauta adandiwuza kuti,
18“Lero mudutsa dziko la Amowabu, podzera njira ya ku Ari.
19Gen. 19.38 Tsono mukadzafika pafupi ndi dziko la Aamoni, musaŵavute kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindikupatsani dziko lao, popeza kuti dzikolo ndidalipereka kwa zidzukulu za Loti, kuti likhale laolao.”
20(Dziko limeneli linalinso dziko la Arefaimu, chifukwa kale iwowo ankakhala m'dziko limeneli. Aamoni ankaŵatchula kuti Azamzumimu.
21Kutalika kwao ankalingana ndi Aanaki. Anali anthu otchuka ndiponso ochuluka kwambiri. Komabe Chauta adaŵaononga, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi Aamoni amene adakhazikika kumeneko.
22Zimenezi ndi zomwe Chauta adaachita ndi zidzukulu za Esau zimene zinkakhala ku Seiri. Iye adaononga Ahori, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi ana a Esauwo, nakhazikika kumeneko, ndipo akukhalako mpaka lero lino.
23Kunena za Avimu amene ankakhala m'midzi yonse mpaka ku Gaza, dziko lao adalilanda ndi Akafitori ochokera ku Kafitori, amene adakhazikika kumeneko ataononga Avimu aja.)
24Tsono Chauta adaonjeza kuti, “Nyamukani tsopano, tiyeni, muwoloke mtsinje wa Arinoni. Ndikukupatsani Sihoni Mwamoriyo, mfumu ya Hesiboni, pamodzi ndi dziko lake lomwe. Mputeni, ndipo muyambepo kumenyana naye nkhondo.
25Ndiyamba lero kuŵachititsa mantha anthu a pa dziko lapansi kuti azikuwopani. Aliyense akangomva za inu, adzanjenjemera ndi mantha ndi kuda nkhaŵa chifukwa choopa inu.”
Aisraele agonjetsa mfumu Sihoni(Num. 21.21-30)26Tsono ndidatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti, kuti apite kwa mfumu Sihoni wa ku Hesiboni. Poŵatumapo, ndidaŵauza kuti akanene mau amtendere, kuti,
27“Tiloleni, tidzere m'dziko mwanu. Tidzangodutsa dziko lanulo molunjika podzera mu mseu osapatuka uku ndi uku.
28Chakudya mudzachita chotigulitsa, madzi akumwanso mudzachita otigulitsa. Mungotilola kuti tidzere m'dziko mwanu,
29kuti tiwoloke mtsinje wa Yordani ndi kukafika ku dziko limene Chauta, Mulungu wathu, akutipatsa. Zidzukulu za Esau ku Edomu, ndi Amowabu ku Ari, onsewo adatilola kudzera m'maiko mwao.”
30Koma mfumu Sihoni yekha sadatilole kuti tidzere m'dziko mwake. Chauta, Mulungu wanu, adamuumitsa khosi nampatsa mtima wouma, kuti ampereke m'manja mwathu monga momwe mukuwonera lero lino.
31Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Taona ndayamba kale kukupatsa mfumu Sihoni ndi dziko lake lomwe. Uyambe kulilandadi, kuti mukakhale ndithu m'menemo.”
32Pamenepo Sihoni pamodzi ndi anthu ake adabwera kudzalimbana nafe pafupi ndi mudzi wa Yahazi.
33Koma Chauta, Mulungu wathu, adampereka kwa ife, ndipo tidamgonjetsa iyeyo pamodzi ndi ana ake ndi anthu ake omwe.
34Tidalandanso ndi kuwonongeratu midzi yake yonse, ndi kupha amuna ndi akazi onse ndi ana omwe. Sitidasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.
35Ng'ombe zokha tidasunga ngati zofunkha zathu, pamodzi ndi chuma cha m'mizinda imene tidalandayo.
36Kuchokera ku Aroere, mzinda umene uli pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, ndiponso kuchokera ku mzinda umene uli m'dambomo mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda wa malinga aatali ndi umodzi womwe umene udatikanika kugwetsa. Chauta adatithandiza kulanda mizinda yonse.
37Koma ku dziko la Aamoni sitidadzereko, ndiye kuti m'mbali mwa mtsinje wa Yaboki kapena kuti mizinda ya ku dziko lamapiri, kapenanso kwina kulikonse kumene Chauta, Mulungu wathu, adaatiletsa kupitako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.