Yes. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lothokozera Mulungu

1Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga.

Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu.

Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa

mokhulupirika ndi motsimikiza,

zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.

2Mzinda uja mwausandutsa mulu wamiyala,

Mzinda wamalinga uja mwausandutsa bwinja.

Nyumba zamphamvu za adani athu si mzindanso tsopano,

sizidzamangidwanso.

3Nchifukwa chake anthu amphamvu a

mitundu yonse adzakutamandani,

m'mizinda ya mitundu yankhalwe anthu adzakuwopani.

4Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka,

mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa

pa nthaŵi yamavuto.

Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe,

ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa.

Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma,

ngati chitungu m'dziko louma.

5Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.

Monga momwe mthunzi wa mtambo umathetsera kutentha,

momwemonso mumaletsa nyimbo ya anthu ankhalwe.

Mulungu akonza phwando

6Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo.

7Pa phiri limeneli adzachotsa chisoni chimene chaphimba anthu a mitundu yonse, chimene chakuta mafuko onse.

81Ako. 15.54; Chiv. 7.17; 21.4Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.

9Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”

Mulungu adzalanga Mowabu

10 Yes. 15.1—16.14; Yer. 48.1-47; Ezek. 25.8-11; Amo. 2.1-3; Zef. 2.8-11 Chauta adzateteza phirili ndi dzanja lake, ndipo Amowabu adzaŵapondereza pomwe aliripo, monga momwe manyowa amaŵaponderezera m'dzenje.

11Amowabuwo adzayesa kutambasula manja ao monga amachitira munthu wosambira. Koma Chauta adzathetsa kudzitama kwao ndiponso luso la manja ao.

12Adzagumula malinga ao ataliatali. Adzaŵagwetsa, kenaka adzaŵaponya pansi, pafumbi penipeni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help