1Kodi wachimwa mwana wanga?
Usachimwenso tsono,
ndipo upemphe chikhululukiro cha zolakwa zako zakale.
2Uzithaŵa tchimo monga m'mene umathaŵira njoka,
chifukwatu tchimo ukaliyandikira limakuluma.
Mano ake ali ngati a mkango,
limalanda moyo wa anthu.
3Kusatsata Malamulo kuli ngati lupanga lakuthwa konsekonse,
limadzetsa chilonda chosapola.
4Kuwopseza ena ndi kuchita nkhanza kumaononga
chuma cha munthu,
choncho nyumba ya munthu wonyada idzapasuka.
5 Mphu. 35.17-19 Kupemphera kwa munthu wosauka kumaŵaloŵa
m'makutu Ambuye,
ndipo amamthandiza msanga.
6Wodana ndi kudzudzulidwa akutsata njira ya anthu ochimwa,
koma aliyense woopa Ambuye
amalapa ndi mtima wonse.
7Munthu wolongolola amadziŵika ponseponse,
koma munthu wanzeru amazindikira kulakwa kwake.
8Munthu womanga nyumba ndi ndalama zobwereka,
ali ngati munthu wodziwunjikira miyala ya pamanda pake.
9Msonkhano wa anthu osasamala Malamulo,
uli ngati mulu wa mapesi,
mathero ake ndi moto ndithu basi.
10Mseu wa anthu ochimwa ngwosalala,
koma kumathero kwake nkumanda.
Za munthu wanzeru ndi munthu wopusa11Aliyense wosunga malamulo,
amatha kulamulira maganizo ake.
Kuwopa Ambuye ndiye chiyambi cha nzeru.
12Munthu wopanda luso sangaphunzitsidwe.
Komabe lilipo luso lina lodzetsa zoŵaŵa.
13Nzeru za munthu waluntha
zili ngati mtsinje wosefukira,
malangizo ake ali ngati kasupe wamoyo.
14Mtima wa chitsiru uli ngati mtsuko wobooka,
susunga zimene waphunzira.
15Munthu wophunzira akamva mau anzeru
amaŵabvomereza,
ndipo amaonjezapo mau ena anzeru.
Koma chitsiru chikamva mau omwewo
sichiŵakonda, chimaŵaponya kumbuyo.
16Mau a chitsiru ngovuta ngati katundu wolemera pa ulendo,
koma kumva nkhani zanzeru kumakondweretsa.
17Pa msonkhano anthu amakonda kumva mau a munthu wanzeru,
ndipo amaŵasinkhasinkha mumtima mwao.
18Nzeru za munthu wopusa zili ngati nyumba yopasuka,
iye amangodziŵa kunena zosokonezeka.
19Kwa munthu wopusa kuphunzira kuli ngati
matangadza m'miyendo,
ngati unyolo ku dzanja lake lamanja.
20Munthu wopusa amaseka mokweza,
koma munthu wochenjera amangoti mwee.
21Kwa munthu wanzeru kuphunzira kuli ngati
makaka agolide,
ngati khoza pa mkono wa ku dzanja lamanja.
22Munthu wopusa amangoti m'nyumba gulupiti,
koma munthu wanzeru amaima panja mwaulemu.
23Munthu wopusa amasuzumira pa khomo,
koma munthu wa mwambo amaima pa khomo.
24Kumamvetsera m'makomo mwa anthu nkupanda
mwambo.
Munthu wanzeru amadziŵa kuti zimenezi
nzochititsa manyazi.
25Akazitape amangobwereza
zimene anthu ena alankhula,
koma anthu anzeru amayamba asanthula mau ao.
26Anthu opusa amayamba nkulankhula asanaganize,
koma anthu anzeru amayamba aganiza asanalankhule.
27Munthu akatemberera mdani wake
ndiye kuti akudzitemberera iye yemwe.
28Kazitape amangodziipitsa yekha,
anthu onse oyandikana naye amadana naye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.