Lk. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ateofilo olemekezeka,

Anthu ambiri adayesa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu.

2Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziwona chamaso kuyambira pachiyambi pake, nakhala akuzilalika.

3Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m'mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane.

4Ndatero kuti mudziŵe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi.

Mngelo aneneratu za kubadwa kwa Yohane Mbatizi

5 Mkazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni.

6Aŵiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo ankatsata mokhulupirika malamulo ndi malangizo onse a Ambuye.

7Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabala, ndipo aŵiri onsewo anali okalamba.

8Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake yaunsembe pamaso pa Mulungu. Inali nthaŵi ya gulu lake la ansembe kutumikira.

9Potsata dongosolo lao la ansembe, iye adaasankhidwa mwamaere kuti akaloŵe m'Nyumba ya Mulungu kukafukiza lubani.

10Khamu lonse la anthu linkapemphera kunja pa nthaŵi yofukiza lubaniyo.

11Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaaimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizirapo lubani.

12Zakariya adadzidzimuka pomuwona, nachita mantha.

13Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.

14“Udzakondwa ndi kusangalala,

anthu ambirinso adzakondwa

chifukwa cha kubadwa kwake,

15 Num. 6.3 popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye.

Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse.

Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera

ngakhale asanabadwe nkomwe.

16Adzatembenuza Aisraele ambiri

kuti abwerere kwa Ambuye, Mulungu wao.

17 Mal. 4.5, 6; Mphu. 48.10, 11 Molimba mtima ndiponso mwamphamvu monga mneneri Eliya,

adzatsogolako Ambuye akubwera.

Adzayanjanitsanso makolo ndi ana ao,

adzatembenuza anthu osamvera

kuti akhale ndi nzeru zonga za anthu olungama.

Adzakonzera Ambuye anthu okonzekeratu kuŵatumikira.”

18Zakariya adafunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingadziŵe bwanji kuti zimenezi nzoona? Ineyo ndine nkhalamba, mkazi wanga nayenso wakalamba.”

19Dan. 8.16; 9.21; Tob. 12.15Mngeloyo adati, “Ine ndine Gabriele, amene ndimakhala kufupi ndi Mulungu. Iyeyo wachita kundituma kuti ndilankhule nawe ndi kukuuza uthenga wabwinowu.

20Iweyo sudakhulupirire zimene ndanenazi, koma zidzachitika ndithu pa nthaŵi yake. Nchifukwa chake udzakhala duu, osatha kulankhula, kufikira tsiku lodzachitika zimenezi.”

21Nthaŵi yonseyo anthu aja ankadikira Zakariya, nkumadabwa kuti akuchedwa m'Nyumba ya Mulungumo.

22Pamene iye adatuluka, sadathe kulankhula nawo. Apo iwo adazindikira kuti m'Nyumbamo waona china chake m'masomphenya. Iye adalankhula nawo ndi manja okha, osathanso kunena mau.

23Atatha masiku ake otumikira m'Nyumba ya Mulungu, adapita kwao.

24Pambuyo pake mkazi wake Elizabeti adatenga pathupi, nabindikira miyezi isanu.

25Adati, “Ambuye andichitira zotere: nthaŵi inoyi andiwonetsa chifundo chao, andichotsa manyazi pakati pa anthu.”

Mngelo Gabriele aneneratu za kubadwa kwa Yesu

26Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete.

27Mt. 1.18Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria.

28Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.”

29Maria adadzidzimuka nawo kwambiri mau ameneŵa, nayamba kusinkhasinkha kuti kodi moni umenewu ndi wa mtundu wanji?

30Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima.

31Mt. 1.21Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu.

32 2Sam. 7.12, 13, 16; Yes. 9.7 “Adzakhala wamkulu,

ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse.

Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide,

33ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya.

Ufumu wake sudzatha konse.”

34Koma Maria adafunsa mngeloyo kuti, “Zimenezi zidzachitika bwanji, popeza kuti sindidziŵa mwamuna?”

35Mngeloyo adayankha kuti,

“Mzimu Woyera adzakutsikirani,

ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani.

Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera,

ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu.

36“Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.

37Gen. 18.14Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”

38Apo Maria adati, “Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo.” Ndipo mngeloyo adamsiya.

39Patapita masiku oŵerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya.

40Adakaloŵa m'nyumba ya Zakariya, malonjera Elizabeti.

41Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera,

42Yud. 13.18ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “Ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwana wanu.

43Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere?

44Chifukwatu pamene ndinamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m'mimba mwanga.

45Ndinu odala chifukwa mudakhulupirira kuti zimene Ambuye adakuuzani, zidzachitadi.”

Nyimbo ya Maria yoyamika Mulungu

46Pamenepo Maria adati,

“Mtima wanga ukutamanda Ambuye,

47ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu,

Mpulumutsi wanga,

48 1Sam. 1.11 popeza kuti wayang'ana kutsika kwa mtumiki wake.

Ndithu kuyambira tsopano

anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala,

49pakuti Iye amene ali wamphamvu wandichitira zazikulu,

ndipo dzina lake nloyera.

50Amaŵachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo

amene amamlemekeza.

51Wachita zamphamvu ndi dzanja lake,

wabalalitsa anthu a mtima wonyada.

52 Yob. 5.11; 12.19; Mphu. 10.14 Mafumu amphamvu waŵatsitsa pa mipando yao yachifumu,

anthu wamba nkuŵakweza.

53Anthu anjala waŵakhutitsa ndi zabwino,

anthu olemera nkuŵabweza osaŵapatsa kanthu.

54Wadzathandiza anthu ake Aisraele,

pokumbukira chifundo chake.

55 Gen. 17.7 1Sam. 2.1-10 Izi ndi zomwe adaalonjeza

kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja,

Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.”

56Maria atakhala ndi Elizabeti ngati miyezi itatu, adabwerera kwao.

Kubadwa kwa Yohane Mbatizi

57Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna.

58Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye amchitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi.

59 Lev. 12.3 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo atabadwa, adadza naye kuti amuumbale, nafuna kumutcha dzina la bambo wake Zakariya.

60Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.”

61Pamenepo anthuwo adamuuza kuti, “Koma pakati pa abale anu palibe amene ali ndi dzina limeneli.”

62Tsono adalankhula ndi bambo wake ndi manja, namufunsa kuti, “Mukufuna kuti timutche dzina lanji?”

63Zakariya adapempha cholemberapo, nalembapo kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo adazizwa.

64Pomwepo Zakariya adathanso kulankhula, nayamba kutamanda Mulungu.

65Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri a ku Yudeya.

66Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m'mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkachita kuwonekeratu kuti Ambuye anali naye.

Nyimbo ya Zakariya

67Tsono Zakariya, bambo wa Yohaneyo, adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Adati,

68“Atamandike Ambuye, Mulungu wa Aisraele,

chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaŵaombola.

69Adautsa wina, wa fuko la mtumiki wake Davide,

kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu.

70Izi ndi zomwe Iye adaaneneratu kalekale

kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.

71Adaalonjeza kuti adzatipulumutsa kwa adani athu,

ndi kwa onse odana nafe.

72Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale,

ndipo wakumbukira chipangano chake choyera.

73Adalonjezanso Abrahamu, kholo lathu, molumbira,

74kuti adzatipulumutsa kwa adani athu,

kuti tizimtumikira mopanda mantha,

75kuti tikhale oyera mtima ndi olungama pamaso pake,

masiku onse a moyo wathu.

76 Mal. 3.1 Tsono mwana iwe,

udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse,

chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye,

kuti ukonzeretu njira zao.

77Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa

pakuŵakhululukira machimo ao.

78Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu,

adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa

kuchokera Kumwamba.

79 Yes. 9.2 Kuŵala kwake kudzaunikira onse

okhala mu mdima wabii ngati wa imfa,

kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”

80Mwana uja Yohane ankakula nasanduka wa mkhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help