Mas. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chithandizoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Kodi mpaka liti, Inu Chauta?

Kodi mudzandiiŵala mpaka muyaya?

Kodi mudzandibisira nkhope yanu nthaŵi zonse?

2Kodi ndizivutika m'maganizo mwanga mpaka liti?

Kodi ndiyenera kukhala ndi chisoni mumtima mwanga

usana ndi usiku?

Kodi mdani wanga azindipambana mpakampaka?

3Mundikumbukire ndipo mundiyankhe,

Inu Chauta, Mulungu wanga.

Mundiwunikire kuti ndingagone tulo tofa nato.

4Mdani wanga asati, “Ndampambana,”

adani anga onse asakondwere poona kuti ndagwa.

5Koma ine ndimadalira chikondi chanu chosasinthika.

Mtima wanga udzakondwera chifukwa mwandipulumutsa.

6Ndidzaimbira Chauta,

popeza kuti wandichitira zabwino.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help