1 Sam. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Bokosi lachipangano pakati pa Afilisti.

1Afilisti atalanda Bokosi lachipangano lija, adalinyamula kuchoka nalo ku Ebenezeri nakafika nalo ku Asidodi.

2Tsono adatenga Bokosilo nakaliika m'nyumba ya Dagoni, mulungu wao, pambali pa Dagoniyo.

3M'maŵa mwake anthu a ku Asidodi atadzuka m'mamaŵa, adangoona Dagoni atagwa chafufumimba patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Apo anthuwo adatenga fanolo, naliikanso pamalo pake.

4Koma m'maŵa mwakenso atadzuka, adangoonanso Dagoni uja atagwa, ali chafufumimba, patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Mutu wa Dagoni ndi manja ake omwe zinali zitaduka ndi kugwera pa chiwundo. Thunthu lake lokha la Dagoniyo ndilo limene lidamutsalira.

5Chimenechi ndicho chifukwa chake chimene ansembe a Dagoni ndi anthu onse amene amaloŵa m'nyumba ya Dagoni, sapondera pa chiwundo cha nyumbayo ku Asidodi, mpaka pano.

6Kenaka Chauta adalanga koopsa anthu a ku Asidodi. Iwowo pamodzi ndi anthu a m'dziko lozungulira adaŵalanga ndi mafundo.

7Anthuwo ataona m'mene zinthu zinaliri, adati, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele lisakhale ndi ife, pakuti Mulungu wao watilanga kwambiri ifeyo ndi mulungu wathu yemwe Dagoni.”

8Choncho adaitana akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, nafunsana kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipangano la Chauta wa Aisraele?” Anthuwo adayankha kuti, “Bokosi limeneli litumizidwe ku Gati.” Motero adatumiza Bokosi lachipanganolo kumeneko.

9Koma atafika nalo ku Gati, Chauta adauvuta mzindawo, ndipo anthu adachita mantha kwambiri. Choncho anthu amumzindamo adazunzika kwabasi, ana ndi akulu omwe, kotero kuti mafundo ankaŵatuluka anthu onsewo.

10Tsono adatumiza Bokosi lachipanganolo ku Ekeroni. Koma litangofika ku Ekeroniko, anthu akumeneko adalira kuti, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele, abwera nalo kwathu kuno, kuti atiphetse ife pamodzi ndi anthu athu.”

11Nchifukwa chake adaitananso akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, ndipo adati, “Chotsani Bokosili, ndipo mulibwezere kumene lidachokera, kuti lingatiphe ife pamodzi ndi anthu athu.” Pakuti munali mantha aakulu zedi mumzinda monsemo. Mulungu ankaŵalanga koopsa anthu akumeneko.

12Anthu amene sadafe, adavutika ndi mafundo, ndipo kulira kwa anthu amumzindamo kudamveka mpaka kumwamba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help