Tob. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zaka zotsiriza za Tobiti

1Tobiti adafa ali ndi zaka 112. Ndipo adamuika mwaulemu kwambiri ku Ninive.

2Anali ndi zaka 62 pamene maso ake adaachita khungu. Atayambanso kupenya, adakhala ndi chuma chambiri. Ankathandiza anthu osauka ndi kumayamika Mulungu, osaleka kutamanda ukulu wake.

3Imfa itayandikira, adaitana mwana wake Tobiyasi namuuza kuti,

4Nah. 1.2—3.19“Mwana wanga, tenga ana ako uthaŵire ku Mediya, popeza kuti ndikukhulupirira kuti zimene Mulungu adanena za Ninive kudzera mwa Nahumu, zidzachitikadi zonse. Zonse zimene aneneri a ku Israele, otumidwa ndi Mulungu, adanena za Asiriya ndi Ninive, zidzachitika ndithu, palibe mau ndi amodzi omwe amene adzapite padera. Nthaŵi yake ikadzafika, zonse zidzachitika. Kudzakhala kwabwino kukhala ku Mediya, osati ku Asiriya kapena ku Babiloni. Ndikudziŵa ndipo ndikutsimikiza kuti zimene Mulungu adaanena, zidzachitikadi zonse. Zidzachitika ndithu, palibe chomwe chidzapite padera.

“Anthu a kwathu ku Israele adzaŵagwira onse nkupita nawo ku ukapolo, kutali ndi dziko labwinoli. Ndipo dziko lonse la Israele lidzakhala chipululu, Samariya ndi Yerusalemu adzaonongedwa, pa kanthaŵi Nyumba ya Mulungu idzaonongedwa ndipo adzaitentha.

5Koma Mulungu adzaŵachitiranso chifundo anthu ake ndi kuŵabwezanso ku dziko la Israele. Iwo adzamanganso Nyumba yake, koma yosakongola ngati yoyamba ija, mpaka nthaŵi yake itafika. Tsono nthaŵiyo itakwana, onse adzabwerako kuukapolo kuja, nadzamanganso Yerusalemu mwaulemerero. Nthaŵiyo Nyumba ya Mulungu idzamangidwanso monga m'mene aneneri a ku Israele adaaneneratu.

6“Anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adzatembenuka mtima ndi kumapembedza Mulungu moona. Adzasiya mafano ao amene adaŵasokeretsa kuti azivomera zabodza.

7Ndipo adzatamanda Mulungu wamuyaya potsata zachilungamo. Aisraele onse amene adzakhale moyo pa nthaŵi imeneyo, nadzakhulupirira Mulungu kwambiri, adzaŵasonkhanitsa pamodzi. Onsewo adzafika ku Yerusalemu kuti adzalandirenso dziko la Abrahamu, ndi kudzakhazikika kumeneko mwaufulu mpaka muyaya. Onse okonda Mulungu moona adzasangalala, koma ochimwa ndi ochita zoipa adzatheratu pa dziko lapansi.

8“Tsopano, ana anga, ndikukulamulani kuti muzitumikira Mulungu moona, ndi kumachita zomkondweretsa.

9Phunzitsani ana anu, kuti azichita zolungama ndi kumathandiza osauka. Azikumbukira Mulungu nthaŵi zonse ndi kumatamanda dzina lake mokhulupirika ndiponso ndi mphamvu zao zonse.

10“Tsono iwe mwana wanga, chokako ku Ninive, usakhalenso kuno. Ukadzangoika mtembo wa mai wako pafupi ndi wanga, nthaŵi yomweyo iwe udzachoke, usadzagonenso kuno. Ine ndikuwona kuti mumzinda muno ndi modzaza ndi zonyansa, ndiponso anthu akungochita zoipa mopanda manyazi. Mwana wanga, ukumbukire zoipa zimene adachita Nadabu kumchita Ahikare, bambo womulera. Paja adaamukakamiza kuti atsikire m'manda ali moyo. Koma Mulungu adambwezera Nadabu zimene iye adati amchite Ahikare. Ahikareyo adaonanso kuŵala kwa dzuŵa, koma Nadabu adagwa mu mdima wamuyaya, chifukwa choti adafuna kupha Ahikare. Tsono popeza kuti ankathandiza osauka, Ahikareyo adapulumuka ku msampha wa imfa, umene Nadabu adaamutchera. Nadabuyo adakodwa mu msampha wake womwe nkufera momwemo.

11Motero ana anga, onanitu zimene zimamuwonekera munthu, akamathandiza osauka. Muwonenso zimene zimamchitikira munthu akakhala wosalungama: zotsatira zake ndi imfa. Koma tsopano mphamvu zanga zatha.” Atatero adamgoneka pabedi pake namwalira, ndipo adamuika mwaulemu.

12Mai wake atamwalira, Tobiyasiyo adamuika pafupi ndi bambo wake. Atatero, iyeyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana, adathaŵira ku Mediya. Adakakhala ku Ekibatana pamodzi ndi Raguele, amfumu akwao.

13Adasamalira makolo a mkazi wake mu ukalamba wao. Iwowo atamwalira, adaŵaika ku Ekibatana ku Mediya, ndipo adaloŵa chuma cha Raguele monga momwe adaachitira ndi chuma cha bambo wake Tobiti.

14Tobiyasi adamwalira ali wolemekezeka, atafitsa zaka 117.

15Adakhala ndi moyo mpaka kuwona mzinda wa Ninive ukuwonongedwa ndi Kiyaksare, mfumu ya ku Mediya. Adaonanso Aninive ogwidwa ku nkhondo akubwera nawo ku Mediya. Choncho adatamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene adaŵachita anthu a ku Ninive ndi a ku Asiriya. Asanafe, anali ndi mwai wosangalala poona kuwonongedwa kwa Ninive. Ndipo adatamanda Ambuye Mulungu nthaŵi zonse. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help