Yes. 40 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mau olimbitsa mtima

1“Atonthozeni mtima,

atonthozeni mtima anthu anga,”

akutero Mulungu wanu.

2“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu.

Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha,

machimo ao akhululukidwa.

Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”

3 Mphu. 48.10; Bar. 5.7; Mt. 3.3; Mk. 1.3; Yoh. 1.23 Lk. 3.4-6 Kukumveka mau akuti,

“Konzani njira ya Chauta m'thengo,

lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.

4Chigwa chilichonse achidzaze,

phiri lililonse ndi gomo lililonse alitsitse.

Dziko lokumbikakumbika alisalaze,

malo azitundazitunda aŵasandutse zidikha.

5Motero ulemerero wa Chauta udzaoneka,

anthu onse adzauwona.

Chauta mwini wake ndiye wanena zimenezi.”

6 Yak. 1.10, 11; 1Pet. 1.24, 25 Kudamveka mau akuti, “Lengeza.”

Ine ndidafunsa kuti,

“Kodi ndilengeze chiyani?”

Mau aja adati,

“Ulengeze kuti anthu onse ali ngati udzu.

Kukongola kwao kuli ngati maluŵa akuthengo.

7Udzu umauma, maluŵa amafota,

Chauta akaziwuzira mpweya wake.

Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.

8Udzu umauma, maluŵa amafota,

koma mau a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”

9Kwera pa phiri lalitali,

iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Yerusalemu.

Ufuule kwamphamvu,

iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Ziyoni.

Kweza mau, usaope.

Uuze mizinda ya ku Yuda kuti,

“Mulungu wanu akubwera.”

10 Yes. 62.11; Chiv. 22.12 Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera

kudzaweruza mwamphamvu,

ndipo akulamulira ndi dzanja lake.

Akubwera ndi malipiro ake,

watsogoza mphotho yake.

11 Ezek. 34.15; Yoh. 10.11 Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa.

Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira.

Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Mulungu Wamphamvuzonse wa Israele

12Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja

ndi chikhatho chake,

kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga

ndi dzanja lake?

Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu?

Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?

13 Aro. 11.34; 1Ako. 2.16 Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta?

Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake?

14Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani,

kuti adziŵe zinthu?

Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama?

Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu?

Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?

15 Lun. 11.22; Mphu. 10.16, 17 Mitundu ya anthu

ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko,

ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo.

M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi.

16Nkhalango ya ku Lebanoni

siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto,

nyama zam'menemo sizingakwanire

kuperekera nsembe yootcha.

17Mitundu yonse ya anthu

si kanthu konse pamaso pa Chauta,

Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.

18 Ntc. 17.29 Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani?

Kodi mungamufanizire ndi chiyani?

19Likakhala fano,

ndi munthu waluso amene amalipanga,

kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide,

nalipangira ukufu wasiliva.

20 Lun. 13.11-19; Yere. 1.8-40 Mmphaŵi wosatha kupeza choperekera nsembe,

amasankhula mtengo umene sudzaola.

Amafunafuna mmisiri woti ampangire fano

limene silingagwedezeke.

21Monga simudadziŵe?

Monga simudamve?

Kodi poyamba ponse sadakuuzeni?

Kodi simudamvetse za kakhazikitsidwe ka dziko lapansi?

22Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye

amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba,

kuseri kwa mlengalenga.

Amaona anthu pansi ngati ziwala.

Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira,

ngati hema lokhalamo anthu.

23Amatsitsa mafumu amphamvu,

olamulira dziko amaŵasandutsa achabechabe.

24Iwo ali ngati mbeu zobzala posachedwa,

kapena zofesa chatsopano,

zongoyamba kumene kuzika mizu.

Mbeuzo Chauta akaombetsa mphepo zimauma,

ndipo mkuntho umaziwulutsa ngati mankhusu.

25Woyera Uja akuti,

“Kodi mungathe kundiyerekeza ndi yani?

Kodi alipo wina wolingana nane?”

26 Bar. 3.34, 35 Yang'anani kumlengalenga.

Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi?

Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo,

ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake.

Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu.

Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.

27Iwe Yakobe, ukulankhuliranji?

Iwe, Israele,

ukuneneranji kuti

Chauta sakudziŵa za mavuto ako,

kapenanso kuti sakusamalapo za iwe?

28Kodi sudziŵa? Kodi sudamve?

Chauta ndiye Mulungu wachikhalire,

Mlengi wa dziko lonse lapansi.

Satopa kapena kufooka,

palibe amene amadziŵa maganizo ake.

29Amalimbitsa ofooka,

ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

30Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka,

ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.

31Koma amene amakhulupirira Chauta

adzalandira mphamvu zatsopano,

adzauluka ngati ziwombankhanga.

Adzathamanga koma osatopa,

adzayenda koma osalefuka konse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help