1 Num. 5.12-15 Usamchitire nsanje mkazi wako womukonda,
kuwopa kuti ungamuphunzitse nzeru zoipa zodzakupweteka.
2Usadzipereke kwa mkazi
kuwopa kuti angakhale ndi ulamuliro pa iwe.
3Usamayendera mkazi wachiwerewere,
ukatero adzakukola m'khwekhwe mwake.
4Usachite chizoloŵezi ndi woimba wachikazi,
kuwopa kuti ungagwidwe m'misampha yake.
5Usayang'anitsitse namwali,
kuwopa kuti ungagwe naye nkulangidwirapo.
6Usadzipereke kwa akazi adama;
ukatero udzaononga chuma chako chonse.
7Usamachita cheucheu m'miseu yamumzinda,
ndipo usamayendayenda m'malo mosapitapita anthu.
8Usayang'anitsitse chiphadzuŵa,
ndipo maso ako asakhale pa mkazi wosakhala wako.
Anthu ambiri adasokera nako kukongola kwa mkazi.
Kukongolako kumautsa chilakolako chonga ngati moto.
9Usadyere pamodzi ndi mkazi wamwini
kapena kumwa naye vinyo,
kuwopa kuti ungatengeke ndi kukongola kwake,
pambuyo pake nkusokonezeka
nugwa m'chiwonongeko.
Za kuzoloŵerana ndi amuna10Usalekane ndi bwenzi wakale,
poti watsopano sangalingane naye.
Bwenzi watsopano ali ngati vinyo watsopano,
akakhalitsa, ndi pamene umamumva bwino.
11Usakhumbire kukhoza kwa munthu woipa,
poti sudziŵa zimene zidzamugwera patsogolo.
12Usasangalale ndi zimene anthu onyoza Mulungu
amakondwera nazo.
Kumbukira kuti asanafe adzalangidwa ndithu.
13Usayandikire munthu
amene ali ndi mphamvu zokupha,
ndipo sudzachita mantha ndi imfa.
Ukamuyandikira, uchenjere zedi,
kuti angakuphe.
Udziŵe kuti ukuyenda pakati pa misampha,
kapena pamwamba pa malinga ankhondo.
14Uyesetse ndi mphamvu zonse kudziŵana ndi anzako,
ndipo uzipempha malangizo kwa anthu anzeru.
15Uzikambirana ndi anthu anzeru,
zokamba zako zonse zizikhudza Malamulo
a Mulungu Wopambanazonse.
16Uzidya ndi anthu abwino,
ndipo uzinyadira kuwopa Ambuye.
17Munthu waluso amadziŵika ndi ntchito zake,
mtsogoleri amadziŵika ndi mau ake anzeru.
18Kazitape ndi munthu woopsa pa mudzi,
munthu wapakamwa anthu amadana naye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.