1Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira
kuti adzandithandize.
Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine,
namva kulira kwanga.
2Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko,
m'chithaphwi chamatope.
Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe,
nandiyendetsa bwino lomwe.
3Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga,
nyimbo yake yotamanda Iye.
Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa,
nadzakhulupirira Chauta.
4Ngwodala munthu amene amadalira Chauta,
munthu amene sapatukira ku mafano
kapena kutsata milungu yonama.
5Inu Chauta, Mulungu wanga,
mwatichitira zodabwitsa zambiri,
mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo.
Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu.
Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo,
sindingathe kuziŵerenga zonse
chifukwa cha kuchuluka kwake.
6 Ahe. 10.5-7 Simudafune nsembe ndi zopereka,
koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera.
Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo.
7Tsono ndidati,
“Ndilipo, ndikubwera,
monga zidalembedwa za ine m'buku la malamulo.
8Ndimakonda kuchita zimene mumafuna,
Inu Mulungu wanga,
malamulo anu ali mumtima mwanga.”
9Ndalalika uthenga wabwino wa chipulumutso chanu
pa msonkhano waukulu.
Sindidatseke pakamwa,
monga mukudziŵa, Inu Chauta.
10Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama.
Ndalankhula za kukhulupirika kwanu
ndi za chipulumutso chanu.
Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu
za chikondi chanu chosasinthika
ndi za kukhulupirika kwanu.
11Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta,
chikondi chanu chosasinthika
ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Pemphero lopempha chithandizo(Mas. 70)12Mavuto osaŵerengeka andizinga,
machimo anga andigwira,
kotero kuti sindingathe kuwona populumukira,
ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga,
ndipo ndataya mtima kotheratu.
13Inu Chauta, pulumutseni.
Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza.
14Anthu ofunafuna moyo wanga,
muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza.
Okhumba kundipweteka,
abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa.
15Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,”
achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera.
16Koma onse okufunafunani
akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu.
Onse okondwerera chipulumutso chanu
azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
17Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa,
koma simunandiiŵale.
Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga.
Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.