Yer. 47 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za chilango cha Afilisti

1 Yes. 14.29-31; Ezek. 25.15-17; Yow. 3.4-8; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-7; Zek. 9.5-7 Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya, onena za Afilisti, Farao asanaononge Gaza.

2Adati,

“Onani m'mene madzi akubwerera kuchokera kumpoto,

adzakhala mtsinje wosefukira ndi wamkokomo.

Adzasefukira m'dzikomo ndi kumiza zonse zokhala m'menemo,

mizinda yonse, ndi anthu onse okhalamo.

Anthu azidzafuula,

onse okhala m'dzikomo azidzalira.

3Adzamva mgugu wa akavalo othamanga,

adzamva phokoso la magaleta ake,

ndi kulira kwa mikombero yake.

Atate sadzaganizirako za ana ao,

adzangokhala ali manja lende!

4Ndithu tsiku lidzafika

limene Afilisti onse adzaonongeka,

tsiku limene adzaphedwe otsala onse

amene ati adzathandize mzinda wa Tiro ndi Sidoni.

Pakuti Chauta adzaononga Afilisti,

onse otsala a ku chilumba cha Krete.

5A ku Gaza adzameta mipala yachisoni,

A ku Asikeloni adzangoti chete.

Inu otsala mwa Afilisti,

kodi ndi mpaka liti mudzakhale mukudzichekacheka

chifukwa cha kulira?

6Mukuti, ‘Ha, Chauta lupanga lili m'manja!

Kodi adzapumula liti?

Aliloŵetse m'chimake,

likhale momwemo, lipumule.’

7Kodi lupangalo lingapumule bwanji

pamene Chauta walipatsa kale ntchito yoti limchitire?

Walituma kuti likalimbane ndi Asikeloni,

kuti likathire nkhondo anthu a m'mbali mwa nyanja.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help