Mas. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lotamanda ChautaSalmo la Davide.

1Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa.

Ndidzaopa yani?

Chauta ndiye linga la moyo wanga,

nanga ndichitirenji mantha?

2Pamene adani ndi amaliwongo anga andiputa kuti andiphe,

adzaphunthwa ndipo adzagwa.

3Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,

mtima wanga sudzachita mantha konse.

Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane,

ine sindidzaleka kukhulupirira.

4Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta,

chinthu chofunika kwambiri,

chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta

masiku onse a moyo wanga,

kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta

ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.

5Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza.

Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake,

adzanditeteza pa thanthwe lalitali.

6Ndidzapambana adani anga ondizungulira,

ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake

ndili kufuula ndi chimwemwe.

Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta.

7Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula,

mundikomere mtima ndi kundiyankha.

8Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.”

Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu.

9Musandibisire nkhope yanu.

Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya,

Inu amene mwakhala mukundithandiza.

Musanditaye, musandisiye ndekha,

Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.

10Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga

andisiye ndekha,

Inu Chauta mudzandisamala.

11Mundiwonetse njira zanu zachifundo,

Inu Chauta,

munditsogolere m'njira yosalala,

chifukwa ndili ndi adani ambiri.

12Musandipereke m'manja mwa adani angawo.

Mboni zonama zandiwukira,

ndipo zimandiwopseza.

13Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta

m'dziko la amoyo.

14Tsono khulupirira Chauta.

Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima.

Ndithu, khulupirira Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help