1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aroni ndi ana ake, pamodzi ndi Aisraele onse, kuti Chauta akulamula kuti,
3‘Mwisraele aliyense akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, ku zithando kapena kunja kwa zithando,
4koma osabwera nayo pa khomo pa chihema chamsonkhano, kuti ikhale mphatso yopereka kwa Chauta, munthuyo wapalamula mlandu wa magazi, chifukwa wakhetsa magazi. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.
5Ndiye kunena kuti Aisraele azitenga nyama zimene akadaphera kwina kwake, afike nazo pamaso pa Chauta kwa wansembe wokhala pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo aziphere pomweko, kuti zikhale nsembe zachiyanjano.
6Ndipo wansembe awaze magazi ake pa guwa la Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Atatero atenthe mafuta ake, kuti atulutse fungo lokomera Chauta.
7Motero nsembe zao asadzapherenso milungu yachabe imene amadziipitsa nayo. Limeneli likhale lamulo lao lamuyaya pa mibadwo yonse.’
8“Uŵauze kuti, ‘Mwisraele aliyense, kapena mlendo amene amakhala pakati pao, wopereka nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse,
9akapanda kubwera nayo pakhomo pa chihema chamsonkhano kudzaipereka pamaso pa Chauta, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’
10 Gen. 9.4; Lev. 7.26, 27; 19.26; Deut. 12.16, 23; 15.23 “Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala pakati pao, akadya magazi, ndidzamfulatira ndi kumchotsa pakati pa anthu anzake.
11Ahe. 9.22 Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi, ndipo ndaŵapereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m'magazimo.
12Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti munthu aliyense mwa inu, kapena mlendo wokhala pakati panu, asadye magazi.
13Ndipo Aisraele onse kapena alendo okhala pakati pao, amene amapha ku uzimba nyama kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuŵakwirira ndi dothi.
14“Pajatu moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwake. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti, ‘Musadye magazi a cholengedwa chilichonse, pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwakemo. Aliyense wodya magazi adzachotsedwa.
15Munthu aliyense wodya chinthu chofa chokha, kapena chojiwa ndi chilombo, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo pambuyo pake adzakhala woyeretsedwa.
16Koma akapanda kuchapa zovalazo, kapena akapanda kusamba thupi lonse, adzasenza machimo ake.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.