1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi za mitengo ina yakunkhalango?
3Kodi mtengo umene uja nkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chokolekapo zinthu zao?
4Ha! Paja ndi nkhuni zosonkhera moto. Tsono moto utapsereza nsonga zake za mtengowo pamodzi ndi mphindikati yake, kodi nkugwira nawonso ntchito ina iliyonse?
5Ngakhale usanapse, sikukadatheka kugwira nawo ntchito. Nanga nanji utapserera ndi moto, adzaugwiritsa ntchito bwanji?
6“Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mtengo wamphesa ndidzauponya m'moto monga momwe ndimachitira mitengo ina yakunkhalango. Momwemonso ndi m'mene ndidzaŵachitire anthu a ku Yerusalemu,
7ndidzaŵalanga. Ngakhale athaŵe moto, motowo udzaŵatenthabe. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵalanga.
8Ndipo dziko laolo ndidzalisandutsa chipululu, chifukwa chakuti iwowo sadakhulupirike. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.