1Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.”
2 Eks. 9.10 Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.
3Pambuyo pake mngelo wachiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake pa nyanja. Pomwepo madzi ake adasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Ndipo zamoyo zonse za m'nyanjamo zidafa.
4 Eks. 7.17-21; Mas. 78.44 Kenaka mngelo wachitatu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mitsinje, ndi pa akasupe a madzi. Pomwepo madziwo adasanduka magazi.
5Tsono ndidamva mngelo wolamulira madzi uja akunena kuti,
“Mwachita chilungamo m'mene mwaweruza motero,
Inu Woyera uja, amene mulipo ndipo munalipo kale.
6Pakuti iwo aja adakhetsa magazi
a anthu a Mulungu, ndi a aneneri,
nchifukwa chake mwaŵapatsa magazi kuti amwe.
Zimenezi ndi zimene zikuŵayenera.”
7Pamenepo ndidamva mau ochokera ku guwa lansembe.
Adati,
“Zoonadi Ambuye, Mulungu Mphambe,
chiweruzo chanu chilichonse nchoona ndi cholungama.”
8Pambuyo pake mngelo wachinai adakhuthulira za mumkhate mwake pa dzuŵa. Nthaŵi yomweyo lidaloledwa kupsereza anthu ndi moto wake.
9Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.
10 Eks. 10.21 Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva.
11Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao.
12 Yes. 11.15 Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chimodzi adakhuthulira za mumkhate mwake pa mtsinje waukulu uja wa Yufurate. Pomwepo madzi ake adaphwa, kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kuvuma.
13Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja.
14Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe.
15 Mt. 24.43, 44; Lk. 12.39, 40; Chiv. 3.3 “Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.”
16 2Maf. 23.29; Zek. 12.11 Pamenepo mizimu ija idasonkhanitsa mafumu aja ku malo amene pa Chihebri amatchedwa “Armagedoni.”
17Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!”
18Chiv. 8.5; 11.13, 19Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi.
19Yes. 51.17Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali.
20Chiv. 6.14Zilumba zonse zidafafanizika, mapiri osaonekanso.
21Eks. 9.23; Chiv. 11.19Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.