1Tsono tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraele onse adasonkhana kuti asale chakudya, kuvala chiguduli ndi kudzithira dothi pa mutu.
2Aisraele atadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina, adaimirira, nayamba kuulula machimo ao ndi zolakwa za makolo ao.
3Anthuwo adaimirira pomwepo, ndipo adamva mau a m'buku la Malamulo a Chauta akuŵaŵerenga nthaŵi yokwanira maora atatu. Pa maora atatu enanso, anthuwo ankaulula machimo ao namapembedza Chauta, Mulungu wao.
4Pa makwerero okhalapo Alevi padaimirira Yesuwa, Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Onsewo ankapemphera mokweza mau kwa Chauta, Mulungu wao.
5Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.”
Pemphero pa kulapa6Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
7Gen. 11.31; 12.1; Gen. 17.5 Inu ndinu Chauta, Mulungu amene mudasankha Abramu, kumtulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, ndi kumutcha dzina loti Abrahamu.
8Gen. 15.18-21 Mudaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa Inu, ndipo mudachita naye chipangano chakuti zidzukulu zake mudzazipatsa dziko la Akanani, la Ahiti, la Aamori, la Aperezi, la Ayebusi ndi la Agirigasi. Mudachitadi zimene mudalonjezazo, pakuti Inu ndinu olungama.
9 Eks. 3.7; Eks. 14.10-12 “Mudaona kuzunzika kwa makolo athu ku Ejipito kuja, ndipo mudamva kulira kwao ku Nyanja Yofiira.
10Eks. 7.8—12.32 Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino.
11Eks. 14.21-29; Eks. 15.4, 5 Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama.
12Eks. 13.21, 22 Munkaŵatsogolera masana ndi mtambo, ndipo usiku munkaŵaunikira ndi moto njira imene ankayendamo.
13Eks. 19.18—23.33 Mudatsika pa phiri la Sinai, ndipo mudalankhula nawo kuchokera kumwamba. Mudaŵapatsa malangizo olungama, malamulo oona, zophunzitsa zabwino ndiponso mau aluntha.
14Mudaŵadziŵitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi lopatulika, ndipo mudaŵapatsa malamulo, malangizo, ndiponso mau anu, kudzera mwa Mose mtumiki wanu.
15Eks. 16.4-15; Eks. 17.1-7; Deut. 1.21 Mudaŵapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye. Mudaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe, kuti aphere ludzu. Mudaŵauza kuti apite kukalanda dziko limene Inu mudaalonjeza kuti mudzaŵapatsa.
16 Num. 14.1-4; Deut. 1.26-33 “Koma makolo athu adadzitukumula nakhala okanika ndipo sadamvere malamulo anu.
17Eks. 34.6; Num. 14.18 Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye.
18Eks. 32.1-4 Ngakhale pamene adadzipangira fano la mwanawang'ombe, namanena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene adatitulutsa ku dziko la Ejipito,’ ndipo ngakhale adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani,
19Deut. 8.2-4 Inu amene muli ndi chifundo chachikulu, simudaŵasiye m'chipululu iwowo. Mtambo umene unkaŵatsogolera poyenda m'njira masana sudaŵachokere, ndipo moto umene unkaŵaunikira njira poyenda usiku sudaŵasiye.
20Inu mudaŵapatsa mzimu wanu wabwino kuti aziŵalangiza. Simudaŵamane chakudya cha mana chija, ndipo mudaŵapatsa madzi akumwa, kuti aphe ludzu lao.
21Mudaŵasunga zaka makumi anai m'chipululu ndipo nthaŵi yonseyo sankasoŵa kanthu. Zovala zao sizidathe, mapazi aonso sadatupe.
22Num. 21.21-35 Mudaŵapatsa mphamvu zogonjetsera maiko ndiponso mitundu ya anthu. Mudaŵagaŵiranso maiko achilendo, ndipo choncho adalanda dziko la Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
23Gen. 15.5; 22.17; Yos. 3.14-17 Mudachulukitsa zidzukulu zao ngati nyenyezi zamumlengalenga. Mudaŵaloŵetsa m'dziko limene mudaauza makolo ao kuti adzalilandira nkukhala lao.
24Yos. 11.23Choncho zidzukulu zaozo zidaloŵamo ndi kukhazikika m'menemo, ndipo Inu mukuŵatsogolera, mudagonjetsa Akanani, nzika za m'dzikomo. Akananiwo, ndiye kuti mafumu ao ndi anthu onse am'dzikomo, mudaŵapereka kwa anthu anu, kuti achite nawo monga angafunire.
25Deut. 6.10, 11 Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta.
26 Owe. 2.11-16 Lun. 2.10-20 “Komabe iwowo sankamvera, ndipo adakuukirani. Adaŵataya kunkhongo Malamulo anu, napha aneneri anu amene ankaŵadzudzula kuti abwerere kwa Inu. Adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani.
27Nchifukwa chake Inu mudaŵapereka kwa adani ao amene ankaŵavuta. Pa nthaŵi imene anali m'mavutoyo, ankalira kwa Inu, ndipo Inu munkaŵamvera muli Kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, mudaŵapatsa atsogoleri amene ankaŵapulumutsa kwa adani ao.
28Koma atakhala pa mtendere, adayambanso kuchimwa pamaso panu, ndipo mudaŵaperekanso kwa adani ao, kotero kuti adani aowo ankaŵalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira Inu, Inuyo munkaŵamvera muli Kumwambako. Motero nthaŵi zambiri munkaŵapulumutsa chifukwa cha chifundo chanu.
29Lev. 18.5 Zoonadi Inu mudaŵachenjeza kuti ayambenso kutsata Malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula, ndipo sankamvera malamulo anu. Adachimwira malangizo anu opatsa moyo kwa anthu oŵasunga. Ankakufulatirani namaumitsa mitu yao, osafuna kumvera.
302Maf. 17.13-18; 2Mbi. 36.15, 16 Mudaŵapirira zaka zambiri ndipo munkaŵachenjeza ndi mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, komabe sadafune kutchera khutu. Nchifukwa chake mudaŵapereka kwa anthu a m'maiko ena.
31Ngakhale zinali choncho, Inu simudaŵaononge kotheratu, kapena kuŵasiya, pakuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo.
32 2Maf. 15.19, 29; 17.3-6; Eza. 4.2, 10 “Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, mumasunga chipangano ndi chikondi chanu chosasinthika. Musalole kuti zosautsa zathu zonse zikuwonekereni ngati zochepa. Zosautsazo zatigwera ife, mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu, ndiponso anthu anu onse, kuyambira nthaŵi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero lino.
33Komabe Inu mwakhala olungama pa zonse zimene zatigwera, ndipo mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa.
34Mafumu athu, akulu athu, ansembe athu ndi makolo athu, sadasunge mau anu, ndipo sadasamale malamulo anu ndi malangizo anu amene mudaŵapatsa.
35Pamene iwo ankadzilamulira okha, namalandira zabwino zanu m'dziko lalikulu ndi lachonde limene mudaŵapatsa, sadakutumikireni, ndipo sadazisiye ntchito zao zoipa.
36Onani, ife ndife akapolo lero lino, ndife akapolo m'dziko limene mudapatsa makolo athu, kuti azidya zipatso zake ndi zabwino zake zonse.
37Tsopano chuma cha dzikolo changolemeza mafumu amene mudaŵaika kuti azitilamulira kaamba ka machimo athu. Ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndiponso ng'ombe zathu monga afunira. Ndithudi, ife tili m'mavuto aakulu.”
Anthu avomera chipangano molemba38Chifukwa cha zonsezi tikuchita chipangano chotsimikizika chichita kulemba, ndipo akuluakulu athu, Alevi athu ndi ansembe athu asindikiza chidindo pa chipanganocho.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.