Lev. 26 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Omvera amadalitsidwa(Deut. 7.12-24; 28.1-14)

1 Lev. 19.4; Eks. 20.4; Deut. 5.8; 16.21, 22; 27.1 “Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

2Muzisunga masiku anga a Sabata ndi kulemekeza malo anga oyera. Ine ndine Chauta.

3 Deut. 11.13-15; 28.1-14 “Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi,

4ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.

5Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani.

6Ndidzabweretsa mtendere m'dziko mwanu, ndipo muzidzagona pansi popanda wokuwopsani. Ndidzapirikitsa zilombo zoopsa m'dziko mwanu, ndipo m'dziko mwanu simudzakhala nkhondo.

7Mudzapirikitsanso adani anu, ndipo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga.

8Anthu asanu okha mwa inu adzapirikitsa anthu zana ndipo anthu zana mwa inu adzapirikitsa anthu zikwi khumi, ndipo adani anuwo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga

9Ndidzakukumbukirani, ndipo ndidzakubalitsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzalimbitsa chipangano changa ndi inu.

10Muzidzadyabe sundwe wakalekale, koma mudzachotsa sundweyo m'khokwe, kuti zatsopano zipeze malo.

11Ndidzakhala pakati panu ndipo sindidzaipidwa nanu.

122Ako. 6.16 Ndidzayenda pakati panu. Ine ndidzakhala Mulungu wanu, inu mudzakhala anthu anga.

13Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo a Aejipito. Ndadula goli lanu kuti muziyenda moongoka.

Za chilango chifukwa chosamvera(Deut. 28.15-68)

14 Deut. 28.15-68 “Koma mukapanda kundimvera ndi kutsata malamulo anga onseŵa,

15mukamanyoza malamulo anga, ndipo mtima wanu ukamadana ndi zimene ndikulamulani, mpaka kusamvera malamulo anga onse ndi kuswa chipangano changa,

16ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya.

17Ndidzakufulatirani, ndipo adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulani, ndipo muzidzangothaŵa popanda wokupirikitsani.

18Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu.

19Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa.

20Nyonga zanu zidzapita pachabe, poti nthaka yanu sidzabala kanthu, ndipo mitengo yake sidzabala zipatso.

21“Tsono mukamayenda motsutsana ndi Ine osandimvera, ndidzabweretsa miliri inanso pa inu, yopambana machimo anu kasanunkaŵiri.

22Ndidzabweretsanso zilombo zolusa pakati panu, zimene zidzakudyerani ana anu, ndi kukuwonongerani ng'ombe zanu. Zilombozo zidzachepetsa chiŵerengero chanu, kotero kuti m'njira zanu simuzidzapita anthu.

23“Mukapanda kubwerera kwa Ine nditakulangani chotere, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine,

24Inenso ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anuwo.

25Ndidzabweretsa lupanga pa inu limene lidzakulangani chifukwa chophwanya chipangano changa. Ndipo mukasonkhana m'mizinda mwanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani m'manja mwa adani anu.

26Ndidzachepetsa buledi wanu wa tsiku ndi tsiku mpaka akazi khumi adzapanga buledi mu uvuni umodzi. Ndipo adzakugaŵirani bulediyo pang'onopang'ono. Choncho mudzadya, koma osakhuta.

27“Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine,

28Inenso ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwiniwake ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu.

29Mudzadya ana anu aamuna, ndipo mudzadyanso ana anu aakazi.

30Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu.

31Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu.

32Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa.

33Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja.

34“Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo.

35Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo.

36Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani.

37Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu.

38Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani.

39Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu.

40“Tsono adzaulula machimo ao ndi machimo a makolo ao chifukwa cha kunyenga kwao kumene adandinyenga nako, ndiponso chifukwa cha kuyenda motsutsana ndi Ine.

41Paja chifukwa cha zimenezo Ine ndidatsutsana nawo ndi kuŵafikitsa ku dziko la adani ao. Tsono mitima yao youma idzadzichepetsa ndi kulola kulangidwa chifukwa cha machimo ao.

42Gen. 28.13, 14; Gen. 26.3, 4; Gen. 17.7, 8 Pamenepo ndidzakumbukira chipangano changa ndi Yakobe, Isaki, ndi Abrahamu, ndipo dzikolo ndidzalikumbukira.

43Koma ayambe aisiya nthaka yaoyo, kuti ikondwerere zaka zoipumuza, pamene dziko lili lopanda anthu, iwo atachoka. Tsono iwo adzalangika chifukwa cha machimo ao, popeza kuti adanyoza zimene ndidaŵalamula, ndipo mitima yao idadana ndi malangizo anga.

44Ngakhale zitachitika zonsezo, pamene ali m'dziko la adani ao, sindidzaŵanyoza ndipo sindidzadana nawo mpaka kuŵaononga kwathunthu ndi kuphwanya chipangano changa ndi iwo, chifukwa Ine ndine Chauta, Mulungu wao.

45Koma poŵachitira chifundo ndidzakumbukira chipangano changa ndi makolo ao amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, mitundu ina ya anthu ikupenya, kuti ndikhale Mulungu wao. Ine ndine Chauta.”

46Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adaika pakati pa Iye mwini ndi Aisraele pa phiri la Sinai, kudzera mwa Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help