Mas. 98 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu, wolamulira dziko lonseSalmo.

1Imbirani Chauta nyimbo yatsopano,

popeza kuti wachita zodabwitsa.

Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

2Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo,

waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse

kuti Iye ndi wolungama.

3Wakumbukira chikondi chake chosasinthika

ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele.

Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi

aona chipulumutso cha Mulungu wathu.

4Fuulirani Chauta ndi chimwemwe,

inu dziko lonse lapansi.

Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.

5Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe,

lizani pangwe ndi nyimbo zokoma.

6Imbirani Chauta Mfumu,

imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.

7Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo,

dziko lifuule pamodzi ndi anthu onse am'menemo.

8Mitsinje iwombe m'manja,

mapiri aimbe pamodzi mwachimwemwe

9pamene Chauta akufika,

popeza kuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,

adzaweruza mitundu yonse mosakondera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help