Yes. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsoka la Yerusalemu

1Ariyele, Ariyele, tsoka kwa iwe,

iwe mzinda umene Davide adamangako zithando zankhondo!

Papite chaka chimodzi kapena ziŵiri,

masiku onse achikondwerero apitirire ndithu,

2pamenepo Mulungu adzauthira nkhondo mzinda wa Ariyele.

Tsono kudzakhala kulira ndi kudandaula,

ndipo mzindawo udzasanduka ng'anjo ya guwa lansembe.

3Monga Davide, Mulungu adzamangako

zithando zankhondo zolimbana ndi mzindawo,

adzauzinga ndi nsanja zankhondo

ndi kumanga mitumbira youthirira nkhondo.

4Tsono iwe Yerusalemu utagwetsedwa,

udzalankhula uli pansi,

mau ako adzamveka uli m'fumbi.

Liwu lako lidzafumira pansi ngati la mzukwa,

mau ako adzamveka ngati onong'ona kuchokera m'fumbi.

5Iwe Yerusalemu, chigulu cha adani

ako chidzamwazika ngati fumbi,

chigulu cha ankhondo ankhanza

chidzabalalika ngati mungu wouluka.

Ndipo mwadzidzidzi ndi mosayembekezeka,

6Chauta Wamphamvuzonse adzakupulumutsa ndi mabingu,

zivomezi ndi phokoso lalikulu.

Adzatumizanso kamvulumvulu, namondwe

ndi malaŵi a moto woononga.

7Tsono chigulu cha mitundu ina yonse

ya anthu othira nkhondo mzinda wa Ariyele,

onse olimbana ndi mzindawo

ndiponso linga lake lamphamvu ndi kuuzinga,

onsewo adzazimirira ngati maloto,

ngati zinthu zoziwona m'masomphenya usiku.

8Chigulu cha mitundu ina yonse

ya anthu othira nkhondo Phiri la Ziyoni

chidzakhala ngati munthu wanjala

wolota kuti alikudya,

koma podzuka, ali nayobe njala,

kapena chidzakhalanso ngati munthu waludzu

wolota kuti alikumwa,

koma podzuka, kum'mero kudakali gwaa.

Anthu anyozera machenjezo

9Mudodome ndipo mukhale ozizwa.

Dzichititseni khungu ndipo mukhalebe osapenya.

Muledzere, koma osati ndi vinyo,

ndipo mudzandire, koma osati ndi chakumwa chaukali.

10 Aro. 11.8 Chauta wakugonetsani tulo tofa nato.

Wakutsekani maso, inu aneneri,

wakuphimbani kumutu, inu olosa.

11Kwa inu zinthu zilizonse zoziwona m'masomphenya zakhala zobisika ngati mau a m'buku lomatirira. Buku limenelo atapatsa wina wodziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, iye adzati, “Sindingathe, chifukwa choti nlomatidwa.”

12Ngati bukulo mupatsa wina wosadziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, adzanena kuti “Sindidziŵa kuŵerenga.”

13 Mt. 15.8, 9; Mk. 7.6, 7 Ambuye adati,

“Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine,

koma mau ao ndi opanda tanthauzo,

ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine.

Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe

malamulo ongoŵaloŵeza pamtima,

malamulo ochokera kwa anthu.

14 1Ako. 1.19 Nchifukwa chake Ine ndidzapitiriza

kuŵachitira zodabwitsa anthu amenewo.

Nzeru za anthu ao anzeru zidzatha,

ndipo kuchenjera kwa anthu ao ochenjera

kudzazimirira.”

Anena za kutsogolo

15Tsoka kwa amene amabisira Chauta maganizo ao,

amene amachita ntchito zao mu mdima,

namaganiza kuti palibe amene akuŵaona

ndi kudziŵa zimene akuchita.

16 Yes. 45.9; Mphu. 33.13; Aro. 9.20 Mwazondotsa zinthu zonse.

Kodi chopambana nchiti,

woumba kapena dothi loumbira?

Kodi chinthu chopangidwa chingauze wochipanga kuti,

“Sudandipange ndiwe?”

Monga chingamuuze kuti,

“Sukudziŵa chimene ukuchita?”

17Pajatu pakangopita kanthaŵi,

nkhalango ya Lebanoni idzasanduka munda wachonde,

ndipo munda wachonde udzasanduka nkhalango.

18Tsiku limenelo agonthi adzamva mau a m'buku,

ndipo anthu akhungu amene ankakhala mumdima,

adzapenya.

19Anthu odzichepetsa

adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Chauta,

ndipo anthu osauka adzakondwa

chifukwa cha Woyera uja wa Israele.

20Koma ankhanza adzatheratu,

oseka anzao adzazimirira,

ndipo opendekera ku zoipa adzaonongedwa.

21Mulungu adzalanga anthu osinjirira anzao,

ndiponso ophophonyetsa anthu ozengedwa mlandu.

Adzalanganso amene amapereka umboni wonama,

kuti anzao osalakwa asaweruzidwe molungama.

22Motero tsono Chauta, Mulungu wa Israele,

amene adapulumutsa Abrahamu pa mavuto,

akunena kuti, “Anthu anga sadzanyozedwanso,

nkhope zao sizidzagwanso ndi manyazi.

23Iwo, ndiye kuti ana ao,

akadzaona zimene ndidachita Ine pakati pao,

adzatamanda dzina langa loyera.

Adzazindikira kuyera kwake

kwa Woyera Uja wa Yakobe,

ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israele.

24Anthu opusa adzapeza nzeru,

onyinyirika adzavomera malangizo.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help