1Chauta adandiwuza kuti, “Tsono iwe mwana wa munthu, ulalikire mapiri a ku Israele, unene kuti, Inu mapiri a ku Israele, imvani uthenga uwu wochokera kwa Ambuye Chauta:
2Paja adani anu adanena kuti, ‘Ha, tsopano dziko lamapiri lakale lija lasanduka lathu.’
3Ndiye tsono iwe ulengeze ndi kuŵauza kuti ‘Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pamene adani anu adakusandutsani chipululu ndi kukuponderezani ku mbali zonse, mpaka inu kukhala m'manja mwa anthu a mitundu ina yonse, anthu ankakunenani ndi kukujedani.
4Nchifukwa chake inu, mapiri a ku Israele, imvani zimene Ine Ambuye Chauta ndikuuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene akhala akuifunkha ndi kuinyoza anthu a mitundu yokuzungulirani.’ ”
5“Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndakhala ndikulankhula ndili ndi mkwiyo woopsa, kuŵaimba mlandu anthu a mitundu ina yonse, makamaka a ku Edomu. Iwoŵa, mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndiponso monyoza, adalanda dziko langa kulisandutsa lao, ndi kutengeratu mabusa ake.”
6“Nchifukwa chake ulengeze za dziko la Israele, ndipo uuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, Ndikulankhula ndi mtima wokwiya kwambiri, chifukwa chakuti mudapirira manyozo ochokera kwa mitundu ina ya anthu.
7Motero ndalumbira ndithu kuti anthu a mitundu yokuzunguliraniyo nawonso adzamva manyozo.
8Koma inu, mapiri a ku Israele, mudzaphukanso nthambi, ndipo anthu anga Aisraele mudzaŵabalira zipatso, poti ali pafupi kubwerera kwao.
9Ine ndikusamala za inu, ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwanso ndi kubzalidwa.
10Ndidzachulukitsa anthu mwa inu ndiponso m'dziko lonse la Israele. M'mizinda mudzakhalanso anthu, ndipo nyumba zonse zimene zidaali mabwinja zidzamangidwanso.
11Ndidzachulukitsa anthu anu pamodzi ndi nyama zomwe. Adzachuluka ndithu ndipo adzabereka ana ambiri. Anthu okhala mwa inu ndidzaŵachulukitsa monga momwe adaliri kale, ndipo ndidzakuchitirani zabwino kuposa kale. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
12Ndidzalola kuti anthu ayende pa inu, ndiye kuti inuyo anthu anga Aisraele. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inuyo mudzakhala chuma chao. Simudzalandanso ana a mtundu wao.”
13“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Anthu ena amanena kuti iwe ndiwe dziko lodya anthu ake, ndiponso lolanda ana a anthu a mtundu wake.
14Sudzadyanso anthu, kapena kulanda ana a mtundu wako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
15Sindidzakulolanso kuti umve manyozo a anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyodola kwao, ndipo sudzaphunthwitsanso anthu a m'dziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Za moyo watsopano wa Israele16Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
17“Munthu iwe, pamene Aisraele ankakhala m'dziko lao, adaliipitsa ndi makhalidwe oipa ndiponso ndi zochita zao. Ndidaona kuti makhalidwe ao anali onyansa pa za chipembedzo, ngati mkazi amene ali kunthaŵi yake.
18Ndidaŵalanga mokalipa chifukwa cha magazi a anthu amene iwo adakhetsa m'dzikomo, ndiponso chifukwa cha mafano amene iwo adaipitsa nawo dzikolo.
19Ndidaŵamwaza pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo ndidaŵabalalitsira ku maiko osiyanasiyana. Ndidaŵalanga potsata makhalidwe ao ndi ntchito zao.
20Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Aŵa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’
21Komabe Ineyo ndinkadera nkhaŵa dzina langa loyera, limene Aisraele adaliipitsa pamene ankakhala pakati pa anthu a mitundu ina kumene adapita.”
22“Nchifukwa chake Aisraelewo uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Zimene nditi ndichite, sindichita chifukwa cha inuyo Aisraelenu ai, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mudaliipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene mudapita.
23Dzina langa lotchuka limene lakhala lonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaonetsa kuti nloyera. Tsono anthu a mitundu inayo atazindikira kuti ndaonetsa kuyera kwa dzina langa mwa inu, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
24Ndidzakutulutsani pakati pa mitundu inayo, ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku dziko lililonse, ndipo ndidzakubwezani ku dziko lanu.
25Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo mudzayera, zonse zokuipitsani zidzachoka. Ndiponso ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse.
26Ezek. 11.19, 20 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.
27Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
28Mudzakhala m'dziko limene ndidapatsa makolo anu. Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
29Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu, ndipo sindidzakugwetseraninso njala.
30Ndidzabereketsa mitengo zipatso zambiri ndipo nthaka idzabala zokolola zambiri, kotero kuti simudzanyozekanso chifukwa cha njala pakati pa anthu a mitundu ina.
31Apo mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa. Mudzachita manyazi chifukwa cha machimo anu ndi zonyansa zimene mudachita.
32Ndiyetu dziŵani kuti sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ai. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Choncho Aisraele inu, chitani manyazi, ndipo mugwetse nkhope chifukwa cha makhalidwe anu oipa.
33“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pamene ndidzachotsa machimo anu, ndidzaikamonso anthu m'mizindamo, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja aja.
34Dziko limene lidaasanduka tsala, anthu azidzalimamonso. Kale aliyense wopita m'njira ankaliwona ngati chipululu, tsopano adzaona kuti nlolimidwa.
35Motero anthu azidzati, ‘Dziko lija lidaali tsalali lasanduka ngati munda wa Edeni. Tsopano mukukhala anthu m'mizinda imene kale idaali mabwinja yosiyidwa ndi yoonongeka. Ndiponso mizindayo tsopano ili ndi malinga olimba.’
36Anthu a mitundu ina amene adatsala pafupi nanu, adzadziŵa kuti Ineyo Chauta ndi amene ndidamanganso mizinda yoonongeka ndi kubzalanso zinthu zatsopano m'dziko losiyidwalo. Ineyo Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi.
37“Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Ndidzaŵalolanso Aisraele kuti andipemphe zimene afuna kuti ndiŵachitire. Ndidzachulukitsa anthu ao ngati nkhosa.
38Adzachuluka ngati nkhosa za ku Yerusalemu zimene ankazipereka kale ku nsembe pa nthaŵi ya chikondwerero. Motero mizinda yao yamabwinja ija idzadzazadi ndi magulu a anthu, ndipo iwowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.