1Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire msanga, ndipo anthu aŵalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu.
2Mupempherenso kuti Mulungu atipulumutse kwa anthu ovuta ndi oipa, pakuti si onse ali ndi chikhulupiriro.
3Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
4Ambuye amatipatsa chikhulupiriro chakuti mukuchita zonse zimene timakuuzani, ndipo kuti mudzazichitabe.
5Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m'chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu.
Aŵachenjeza kuti azigwira ntchito6Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.
7Paja inu nomwe mukudziŵa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsanzira. Ife sitinali aulesi pamene tinali pakati panu.
8Sitidalandire chakudya kwa munthu aliyense osalipira, koma tidagwira ntchito kwambiri usana ndi usiku mpaka kutopa, kuwopa kuti tingalemetse wina aliyense mwa inu.
9Sitidachitetu zimenezi chifukwa choti tilibe mphamvu zopemphera chithandizo kwa inu, koma tinkafuna kukhala chitsanzo choti muzichitsanzira.
10Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.
11Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu ameneŵa sagwira ntchito konse, koma amangoloŵera pa za anzao.
12M'dzina la Ambuye Yesu Khristu tikuŵalamula ndi kuŵachenjeza anthu otere kuti azigwira ntchito mwabata, ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito.
13Koma inu abale, musatope nkuchita zabwino.
14Ngati wina aliyense akana kumvera mau amene talemba m'kalatayi, mumuwonetsetse ameneyo, ndipo musayanjane naye, kuti choncho achite manyazi.
15Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale.
Mau otsiriza16Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17Ndi dzanja langa ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine, Paulo.” Mauŵa ndi chizindikiro changa m'kalata iliyonse. Ndimalemba motero.
18Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima nonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.