1Njala idakula kwambiri m'dziko la Kanani.
2Tsono banja la Yakobe lija litadya tirigu yense amene adaakasuma ku Ejipito uja, Yakobe adauza ana ake aja kuti, “Pitaninso, mukatigulireko chakudya pang'ono.”
3Apo Yuda adati, “Munthu uja adatichenjeza kolimba kuti sadzatilola kuwonekera pamaso pake, tikapanda kupita naye mng'ono wathuyu.
4Mukatilola kuti timtenge, tipita kukakugulirani chakudya.
5Mukapanda kulola, ife sitipita, popeza kuti munthu ameneyo adaneneratu kuti, ‘Sindidzakulolani kufika pamaso panga mukapanda kubwera naye mbale wanuyo.’ ”
6Apo Israele adati, “Chifukwa chiyani mudathinitsa zinthu pa ine pomuuza kuti muli ndi mbale wanu winanso?”
7Iwo adayankha kuti, “Ndiye kuti munthuyo ankangofunsitsa za ife ndi za banja lathu nkumati, ‘Kodi bambo wanu akali moyo? Kodi muli naye mbale wanu wina?’ Tsono ife tidaayenera kuyankha mafunso onseŵa. Nanga ife tikadadziŵa bwanji kuti iye atiwuza zoti mbale wathuyo tipite naye limodzi.”
8Yuda adauza bambo wake Israele kuti, “Mnyamatayu patsani ine, ndipo tikonzeke kuti tinyamuke tizipita. Motero tonsefe, inuyo, ana athu pamodzi ndi ife, sitidzafa ndi njala.
9Ine ndikhale ngati chikole cha moyo wake wa Benjamini. Ngati sindidzabwerera naye kuno ali moyo, inu mudzandiimbe mlandu moyo wanga wonse.
10Tikadapanda kuzengereza, tikadapita ndi kubwerako kaŵiri konse tsopano.”
11Tsono bambo wao Israele adaŵauza kuti, “Ngati ndi m'mene ziliri, chitani choncho. Munthuyo mtengereniko zipatso zokoma za dziko lino m'matumba mwanu kuti mukampatse. Mumtengerenso mafuta opaka pang'ono, uchi pang'ono, mafuta onunkhira osiyanasiyana, mure, mtedza, ndiponso zipatso zinanso.
12Mutenge ndalama zokwanira, kuti mukabweze ndalama zomwe zidapezeka m'matumba mwanu zija. Makamaka zinthu zinali zitalakwika.
13Mtengeni mbale wanuyu, ndipo nyamukani, mupitenso kwa munthuyo.
14Mulungu Mphambe akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo, kuti abweze mbale wanu wina uja pamodzi ndi Benjamini. Ngati ana anga onse andifera, andifera ndithu basi.”
15Motero abale onse aja adatenga mphatso zija, ndipo adatenganso ndalama moŵirikiza, namtenganso Benjamini. Tsono adakonzeka, nanyamuka ulendo kupita ku Ejipito. Kumeneko adakaonekera pamaso pa Yosefe.
16Yosefe ataona Benjamini, adauza wantchito woyang'anira zonse panyumba pake kuti, “Anthu aŵa aloŵetse m'nyumba. Ndipo uphe nyama ndi kuiphika bwino, chifukwa anthu ameneŵa adya ndi ine masana ano.”
17Wantchitoyo adachita monga momwe Yosefe adamuuzira, napita nawo abale aja kunyumba kwa Yosefe.
18Koma iwowo adachita mantha kwambiri poona kuti akupita nawo kunyumba kwa Yosefeyo: ankaganiza kuti, “Akutiloŵetsa muno chifukwa cha ndalama zija zidabwezedwa m'matumba mwathu pa nthaŵi yoyamba ija. Akungofuna danga loti achite nafe nkhondo mwadzidzidzi, chifukwa akufuna kutisandutsa akapolo ake ndi kutilanda abulu athuŵa.”
19Motero asanaloŵe m'nyumbamo adafika kwa wantchito wa Yosefe woyang'anira nyumba uja,
20namuuza kuti, “Pepani bwana, ife tidaabweranso kuno kale kudzagula chakudya.
21Titafika pa malo a chigono, pomasula matumba athu, aliyense mwa ife adapeza ndalama zake kukamwa kwa thumba lake, ndipo ndalamazo zinalipo zonse monga momwe tidaaŵerengera. Ndalama zimenezo tabwera nazo.
22Ndipo tabwera nazonso ndalama zina zodzagulira chakudya china. Amene adaika ndalama m'matumba mwathu, sitikumudziŵa ai.”
23Wantchito uja adati, “Musade nkhaŵa, mitima yanu ikhale pansi. Mulungu wanu, Mulungu wa atate anu, ndiye amene adakuikirani ndalama zanu m'matumbamo. Ndalama zanu zoyamba zija ndidalandira.” Atatero, adaŵatulutsira Simeoni uja.
24Wantchitoyo atabwera nawo abalewo m'nyumba mwa Yosefe, adaŵapatsa madzi kuti asambe mapazi ao, ndipo abulu ao aja adaŵadyetsanso.
25Tsono abalewo adakonzeratu mphatso zao zija kuti apereke kwa Yosefe masana, chifukwa anali atamva kuti akadya kumeneko.
26Yosefe atabwera, abale akewo adapereka mphatso zija kwa iye, ndipo adamuweramira.
27Iye adaŵafunsa m'mene aliri, naŵafunsanso kuti, “Kodi bambo wanu wokalamba uja munkandiwuzayu ali bwanji? Kodi akali moyo?”
28Iwowo adayankha kuti, “Mtumiki wanu akali moyo, ndipo ali bwino.” Tsono onsewo adamgwadiranso namuŵeramira pomwepo.
29Yosefe ataona Benjamini, mng'ono wake weniweni uja, adati “Uyu ayenera kukhala mng'ono wanu wotsiriza uja munkandiwuzayu. Mulungu akudalitse, mwana wanga.”
30Atanena zimenezo Yosefe adachokapo mofulumira chifukwa choti mtima wake udaadzaza ndi chifundo chifukwa cha mng'ono wake uja. Anali pafupifupi kulira, motero adapita m'chipinda mwake nakalirira m'menemo.
31Atapukuta m'maso adatuluka, ndipo adalimbanso mtima, nalamula kuti chakudya chibwere.
32Yosefe ankadyera payekha, abale akewo ankadyera pa tebulo lina. Aejipito amene anali naye m'nyumba nawonso ankadyera paokha, chifukwa iwo ankanyansidwa kudyera pamodzi ndi Ahebri.
33Abalewo adaakhala pa tebulo patsogolo pa Yosefe, ndipo anali ataŵaika motsatana ndi kubadwa kwao, kuyambira wamkulu mpaka wamng'ono. Abale aja ataona m'mene aŵakhazikira, adadabwa kwambiri namapenyetsetsana.
34Chakudya chomwe ankadyacho chinkachokera patebulo pa Yosefe, koma chakudya chopatsa Benjamini chinkaposa cha onsewo kasanu. Motero onsewo adadya ndi kumwa pamodzi ndi Yosefe mpaka kukhuta, ndipo adasangalala pamodzi naye.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.