1Munthu wochita liwuma kwina atamdzudzula,
adzaonongeka mwadzidzidzi osachiranso.
2Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa,
koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula.
3Wokonda nzeru amasangalatsa atate ake,
koma amene amayenda ndi akazi adama
amamwaza chuma chake.
4Mfumu imalimbitsa dziko pakuweruza molungama,
koma imene imaumiriza anthu kuti aipatse ziphuphu,
imaononga dziko.
5Munthu amene amathyasika mnzake
amadzitchera msampha yekha.
6Munthu woipa amakodwa ndi zolakwa zake,
koma wochita chilungamo
amakhala wokondwa ndi womasuka.
7Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka,
koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
8Anthu onyoza akhoza kuyatsa mzinda,
koma anthu anzeru amabweza ukali.
9Munthu wanzeru atatsutsana ndi chitsiru,
chitsirucho chimangochita phokoso nkumaseka,
ndipo sipakhala mtendere.
10Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wosalakwa,
koma anthu angwiro amateteza moyo wake.
11Wopusa amaonetsa mkwiyo wake,
koma munthu wanzeru amadzigwira.
12Wolamula akamamvera zabodza,
nduna zake zonse zidzakhala zoipa.
13Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake
amafanafana pa ichi,
chakuti onsewo Chauta ndiye adaŵapatsa maso.
14Mfumu ikamaweruza osauka mosakondera,
ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya.
15Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru,
koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.
16Oipa akamalamulira, zolakwa zimachuluka,
koma ochita chilungamo adzaona kugwa kwa oipawo.
17Uzimlanga mwana wako
ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima,
adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
18Kumene kulibe mithenga yochokera kwa Mulungu,
anthu saweruzika,
ndi wodala munthu amene amatsata malamulo.
19 Mphu. 33.25-30 Munthu wotumikira samulanga ndi mau chabe,
ngakhale aŵamvetse mauwo, sadzasamalako.
20Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi
pali chikhulupiriro,
koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
21Amene amasasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,
pomaliza pake adzapeza kuti kapoloyo
wasanduka mloŵachuma wake.
22Munthu wamangaŵa amautsa mikangano,
munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.
23Kunyada kwa munthu kudzamtsitsa,
koma amene ali wodzichepetsa adzalandira ulemu.
24Woyenda ndi mbala ndi wodana ndi moyo wake,
amamva kutemberera, koma osaulula kanthu.
25Kuwopa anthu kuli ngati msampha,
koma wodalira Chauta amakhala pabwino.
26Ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira aŵakomere mtima,
koma munthu amamuweruza molungama ndi Chauta yekha.
27Anthu osoŵa chilungamo
amanyansa anthu ochita chilungamo,
monga momwe anthu abwino
amanyansira anthu oipa mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.