Yob. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Zofari wa ku Naama adayankha kuti,

2“Iwe Yobe, wandipsetsa mtima.

Nchifukwa chake ndikufulumira kuyankha.

3Ndikumva mau ondidzudzula ndi ondinyoza,

koma ndadziŵa kale m'mene ndingathe kuyankhira.

4Kodi sukudziŵa zimene zidachitika masiku amakedzana,

kuyambira nthaŵi imene munthu adalengedwa pa dziko.

5Kodi sukudziŵa kuti

kukondwera kwa woipa nkosakhalira kutha?

Kodi sukudziŵa kuti

chimwemwe cha munthu wopanda Mulungu

ncha kanthaŵi chabe?

6Ngakhale mbiri yake ifalikire ponseponse,

ndipo ulemerero wake ukwere kufikira ku mlengalenga,

7adzatheratu monga momwe imatayikira ndoŵe yake.

Amene ankamuwona azidzafunsa kuti,

‘Kodi uje uja ali kuti?’

8 Lun. 5.14 Adzangozimirira ngati maloto, ndipo sadzapezekanso.

Adzachotsedwa ngati zinthu zoonekera anthu kutulo usiku.

9Amene adamuwona kale sadzamuwonanso,

sadzapezekanso kunyumba kwake.

10Ana ake adzabwezera zonse,

zimene iyeyo adalanda anthu osauka.

11Thupi lake ndi la nyonga zaunyamata,

komabe nyongazo zidzatha naye limodzi m'fumbi.

12“Zoipa zimakhala zozuna kwa iye,

nchifukwa chake amachita ngati kuzisunga m'kamwa mwake.

13Ngakhale safuna kuleka kuzivumata,

nangozisunga m'kamwa mwakemo,

14zoipazo akazimeza, zimaloŵa m'mimba mwake.

Zimasanduka ngati ndulu ya mphiri m'kati mwa iyeyo.

15Amapeza chuma, koma amachisanzanso.

Mulungu amachitulutsa m'mimba mwa munthuyo.

16Zimene amadya zili ngati ululu wa mphiri,

ndipo ululuwo udzamupha.

17Sadzaona mitsinje ya mafuta a olivi,

kapena mifuleni ya madalitso a m'dziko lamwanaalirenji.

18Adzabweza zimene adapata pogwira ntchito.

Sadzadyerera chuma chake.

Sadzapeza mpata wokondwerera phindu la malonda ake.

19Pakuti adapondereza amphaŵi ndi kuŵasiya osaŵasamala,

ndipo adalanda nyumba zimene sadamange ndiye.

20“Chifukwa choti umbombo wake unali wosakata,

sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.

21Iyeyo ankati akadya, ankadyeratu zonse,

tsono chuma chake chidatheratu.

22Ngakhale ndi wachuma, adzakhala mmphaŵi.

Mavuto aakulu adzamgwera.

23Pa nthaŵi yoti adyerere chuma china,

Mulungu adzamgwetsera ukali wamoto ngati mvula yosakata.

24 Lun. 5.17-23 Adzathaŵa mkondo wachitsulo,

koma adzalasidwa chipyoza ndi muvi wamkuŵa.

25Muviwo atautulutsa m'thupi mwake,

atachotsa nsonga yake yonyezemira yobaya ndulu yake,

iyeyo adzagwidwa ndi mantha aakulu.

26Zonse zimene adazipeza, zazimirira ngati mu mdima.

Moto wopanda woukwereza wamupsereza,

watentha iyeyo pamodzi ndi zonse

zotsalira m'nyumba mwake.

27Zamumlengalenga zidzaulula zolakwa zake,

za pansi pano zidzamuukira.

28Chigumula cha madzi chidzaononga nyumba yake.

Katundu wake yense adzachotsedwa

pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu.

29Izi nzimene Mulungu amasungira munthu woipa.

Ndizo zimene Mulungu adalamula kuti

zikhale mphotho ya munthuyo.”

Yobe

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help