Yos. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu alamula Yoswa kuti agonjetse Kanani.

1Mose, mtumiki wa Chauta, atamwalira, Chauta adalankhula ndi mthandizi wake wa Moseyo, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, kuti,

2“Mose, mtumiki wanga, wafa. Tsono iwe, konzeka tsopano pamodzi ndi Aisraele onseŵa, muwoloke mtsinje wa Yordaniwu, ndipo muloŵe m'dziko limene ndikuŵapatsalo.

3Deut. 11.24, 25 Paliponse pamene muponde phazi lanu, ndakupatsani inu, monga momwe ndidalonjezera Mose.

4Kuyambira ku chipululu kumwera, mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kuvuma, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yaikulu kuzambwe, lonseli lidzakhala dziko lanu.

5Deut. 31.6, 8; Ahe. 13.5 Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse.

6Deut. 31.6, 7, 23 Ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima, chifukwa udzatsogolera anthu ameneŵa pokalandira dziko limene ndidalonjeza kwa makolo ao.

7Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.

8Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

9Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Yoswa alamula anthu.

10Pamenepo Yoswa adalamula atsogoleri a Aisraele naŵauza kuti,

11“Pitani ku zithando zonse, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu, chifukwa atapita masiku atatu, mudzaoloka Yordani ndi kulandira dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.’ ”

12 Num. 32.28-32; Deut. 3.18-20; Yos. 22.1-6 Ndipo Yoswa adauza fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti,

13“Kumbukirani zija zimene Mose, mtumiki wa Chauta, adakuuzani, kuti, ‘Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani dziko limeneli kuti likhale lanu.’

14Tsono akazi anu pamodzi ndi ana anu atsalire m'dziko lino la kuvuma kwa Yordani limene Mose adakupatsani. Ng'ombe zanu zitsalenso, koma ankhondo okha pakati panupa ndiwo aoloke atatenga zida, apite kutsogolo kwa Aisraele anzanu kuti akaŵathandize.

15Ndipo iwowo akadzalandira dzikolo ndi kukhazikikamo, pamenepo ndiye inu mudzabwerere ndi kudzakhala m'dziko lanu limene adakupatsani Mose, mtumiki wa Chauta, konkuno kuvuma kwa Yordani.”

16Onsewo adayankha Yoswa kuti, “Zonse zimene mwatilamulazi tidzachita, ndipo kulikonse kumene mudzatitume, tidzapita.

17Tidzakumverani monga momwe tidamverera Mose. Chauta, Mulungu wanu, akhale nanu, monga momwe adakhalira ndi Mose!

18Aliyense wokangana ndi inu kapena wosamvera malamulo anu, adzaphedwa. Inu mukhale amphamvu, ndipo mulimbe mtima kwambiri.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help