Deut. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chaka cha kumasulidwa(Lev. 25.1-7)

1Chikatha chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse, muzikhululukira onse amene adakongola zinthu zanu.

2Zimenezi zizichitika motere: aliyense amene adakongoza Mwisraele mnzake ndalama, afafanize ngongole imeneyo. Asamuumirize kapena mbale wake kuti abweze ndalamazo, popeza kuti Chauta walamula kuti ngongoleyo ifafanizidwe.

3Mungathe kulonjerera ngongole kwa mlendo yekha, koma ngongole ya munthu wa mtundu wanu muifafanize.

4Palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mtundu wanu amene adzasauke, (poti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko limene Iye adzakupatsani ngati choloŵa chanu,)

5malinga mukamamvera mau ake ndi kusamala zotsata malamulo amene ndikukulamulani leroŵa.

6Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu.

7 Lev. 25.35 Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja.

8Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire.

9Musadzakhale ndi maganizo achabe akuti, “Chaka chofafaniza ngongole chili pafupi.” Mukapanda kumuwonetsa mtima wachifundo mbale wanu wosaukayo, osampatsa kanthu, iyeyo adzakunenezani kwa Chauta molira, ndipo mudzapezeka olakwa.

10Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

11Mt. 26.11; Mk. 14.7; Yoh. 12.8 Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo.

Za m'mene azidzaŵachitira akapolo(Eks. 21.1-11)

12 Lev. 25.39-46 Muhebri mnzanu, mwamuna kapena mkazi, akadzigulitsa kwa inu kuti akhale kapolo wanu, mummasule atangokutumikirani zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, mumlole kuti apite mwaufulu.

13Mukammasula, musangomchotsa ali chimanjamanja.

14Mpatseniko momkomera mtima zonse zimene Chauta adakudalitsa nazoni monga: nkhosa, tirigu ndi vinyo.

15Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani. Nchifukwa chake ndikukupatsani lamulo limeneli tsopano lino.

16Koma kapoloyo akakhala kuti akukukondani inu ndi banja lanu, chifukwa mukukhala naye bwino, mwina sangafune nkuchoka komwe. Ngati zili choncho,

17mutenge zingano ndipo muboole khutu la kapoloyo, mpaka zinganoyo iloŵe m'chitseko. Mukatero, adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Ngati ndi kapolo wamkazi, mudzamchite chimodzimodzi.

18Kumasula kapolo, kuti akhale mfulu, kusakuipireni. Adakutumikirani kale zaka zisanu ndi chimodzi pa theka la mtengo wa wantchito wolembedwa. Chitani zimenezi, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

Ana oyamba kubadwa a zoŵeta

19 Eks. 13.12 Ana onse amphongo oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina, muŵapatule kuti akhale a Chauta, Mulungu wanu. Ng'ombe zimenezi musazigwiritse ntchito, ndipo nkhosazo musazimete bweya.

20Chaka ndi chaka inu, pamodzi ndi banja lanu, muzidya zimenezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ndiponso ku malo amene Chauta adzasankhe.

21Koma ngati pali kanthu kolakwika pa nyamayo, monga kutsimphina kapena khungu, kapena chilema chilichonse, musaphere nsembe Chauta nyama yoteroyo.

22Nyama zotero, mudyere kwanu. Nonsenu, kaya ndinu oyeretsedwa pa za chipembedzo kapena ai, mungathe kudya zimenezo, monga momwe mumadyera mphoyo kapena ngondo.

23Gen. 9.4; Lev. 7.26, 27; 17.10-14; 19.26; Deut. 12.16, 23 Magazi okha musadye, koma mungoŵataya pansi ngati madzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help