1“Tsono upange guwa lofukizirapo lubani. Upange guwalo ndi matabwa a mtengo wa kasiya.
2Likhale lalibanda, kutalika kwake masentimita 46, muufupi mwake likhalenso masentimita 46, ndipo msinkhu wake ukhale wa masentimita 91. Nyanga zake zipangidwire kumodzi ndi guwalo.
3Ulikute ndi golide pamwamba pake, pa mbali zake zonse zinai ndi pa nyanga zakezo. Ndipo kuzungulira guwa lonselo ulembe mkombero wagolide.
4Upange mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo uzilumikize ku guwa m'munsi mwa mkombero pa mbali ziŵiri, kuti mphiko zipisidwe m'mphetezo.
5Mphiko zimenezi ikhale ya mtengo wa kasiya, ndipo uikute ndi golide.
6Guwalo ulikhazike patsogolo pa nsalu yochinga bokosi lachipangano, patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa bokosi lachipangano. Pa malo ameneŵa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
7M'maŵa mulimonse Aroni azifukiza lubani wa fungo lokoma, ndipo nthaŵi yomweyo azikonza nyale zija.
8Tsono pamene ayatsa nyalezo madzulo, azifukizanso lubani. Choncho pakhale kufukiza kosalekeza pamaso pa Chauta m'mibadwo yanu yonse.
9Paguwapo usafukizepo lubani wosaloledwa, kapena zopereka za nyama yopsereza kapena za zakudya. Usadzaperekenso pamenepo chopereka cha chakumwa.
10Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.”
Za chopereka choombolera moyo11Chauta adapitiriza kuuza Mose kuti,
12“Ukamachita kalembera wa ana aamuna a Aisraele, munthu aliyense adzapereke kwa Chauta choombolera moyo wake, kuti mliri uliwonse usadzamugwere pamene kalemberayo akuchitika.
13Eks. 38.25, 26; Mt. 17.24 Aliyense woyenera kulembedwa m'kalemberamo adzapereke theka la sekeli, ndiye kuti ndalama zolemera ngati magaramu asanu ndi limodzi, kutsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu (paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi aŵiri). Ndalama zimenezi zidzakhala zopereka kwa Chauta.
14Aliyense wolembedwa m'kalemberamo, wa zaka makumi aŵiri kapena kupitirira, adzapereke zimenezi kwa Chauta.
15Wolemera asadzapereke kopitirira, ndipo wosauka asadzapereke mochepera pa theka la sekeli, pamene muzikapereka kwa Chauta zopereka zimenezi, kuti muwombole moyo wanu.
16Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.”
Za beseni lamkuŵa17Tsono Chauta adauza Mose kuti,
18Eks. 38.8 “Upange beseni lamkuŵa losambira, ndipo phaka lake likhale lamkuŵa. Ulikhazike pakati pa chihema chamsonkhano ndi guwa, ndipo uthiremo madzi.
19Aroni ndi ana ake azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi ao ndi madzi amenewo.
20Akamaloŵa m'chihema chamsonkhano, kapena kuyandikira guwalo pa ntchito yao yautumiki, ndi kumapereka kwa Chauta chopereka chopsereza, sadzafa malinga akasamba ndi madzi amenewo.
21Azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi, kuti angafe. Limeneli ndi lamulo ndithu limene iwowo ndi adzukulu ao akutsogolo ayenera kumadzalitsata mpaka muyaya.”
Za mafuta odzozera ndi zofukiza22 Eks. 37.29 Chauta adauzanso Mose kuti,
23“Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino,
24makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi.
25Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.
26Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano,
27tebulo ndi zipangizo zake zonse, choikaponyale pamodzi ndi zida zake, guwa lofukizirapo lubani,
28guwa lopserezapo zopereka, pamodzi ndi zipangizo zake, ndiponso beseni losambiramo lija ndi phaka lake lomwe.
29Zonsezi udzazipatula mwa njira imeneyi, ndipo zidzakhala zoyera kopambana. Ndipo chilichonse chokhudza zimenezi chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.
30Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira.
31Tsono Aisraele onse udzaŵauze kuti, ‘Ameneŵa ndiwo adzakhale mafuta anga oyera odzozera pa mibadwo yanu yonse.
32Musadzadzozere anthu wamba, ndipo musadzapangenso mafuta ena ofanafana nawo. Ameneŵa ngoyera ndipo kwa inu adzakhalabe oyera ndithu.
33Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ”
Mapangidwe a lubani34Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge miyeso yofanafana ya zonunkhira bwino izi: sitakate, onika, galibanumu, ndi lubani weniweni.
35Uphatikize pamodzi zonsezi, ndipo upange lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athiremo mchere, ndipo akhale woyera ndi wopatulika.
36Upere gawo lina mosalala kwambiri, ndipo utatapako pang'ono, uike patsogolo pa bokosi lachipangano m'chihema chamsonkhano chokumanirako ndi anthu anga. Lubani ameneyu kwa inu akhale woyera kopambana.
37Ndipo lubani amene upangeyo potsata mapangidwe ake, asadzakhalire inuyo ai, koma adzakhale woyera wokhalira Chauta yekha.
38Ngati munthu wina apanga lubani wofanafana ndi ameneyu kuti amve fungo lake lokoma, azichotsedwa pakati pa anthu anzake.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.