1 Am. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yudasi Makabeo afa ku nkhondo

1Demetriyo atamva kuti Nikanore ndi ankhondo ake adaphedwa ku nkhondo, adatumanso Bakide ndi Alikimo ku Yudeya pamodzi ndi chigawo champhamvu cha gulu lake lankhondo.

2Adadzera mseu wopita ku Galileya, namanga zithando zao zankhondo ku Masaloti ku dziko la Aribela. Adalanda mzindawo, napha anthu ake ambiri.

3Mwezi woyamba wa chaka cha 152, adamanga zithando zao zankhondo pafupi ndi Yerusalemu.

4Kenaka adanyamuka napita ku Beerizeti ndi asilikali oyenda pansi 20,000 ndi okwera pa akavalo 2,000.

5Yudasi adamanga zithando zake zankhondo ku Elasa, ali ndi anthu osankhidwa 3,000.

6Ataona unyinji wa adaniwo, anthu a Yudasi adachita mantha, ambiri nkuthaŵa mozemba, mwakuti adangotsala anthu 800 okha.

7Yudasi adataya mtima poona kuti gulu lake lankhondo labalalika. Nkhondo inali pafupi kuyamba, ndipo panalibenso nthaŵi yosonkhanitsa ankhondo ake.

8Anali wolefuka, komabe adauza otsalawo kuti, “Tiyeni tinyamuke, tikakumane nawo adani athuwo ndi kuwona ngati tingathe kumenyana nawo.”

9Ankhondowo adayesa kumuletsa, adati, “Sitingathe. Chilipo tsopano nchakuti tingopulumutsa moyo wathu. Tidzachite kubweranso pamodzi ndi abale athu aja kuti tidzamenyane nawo, ifeyo ndiye tachepa.”

10Yudasi adaŵauza kuti, “Pasadzakhale wina munthu wonena kuti ine ndathaŵa nkhondo. Ngati nthaŵi yathu yafika, tifere abale athu ndi mtima wopanda mantha, koma tisalole kuti mbiri yathu iipe.”

11Gulu lankhondo la adani lidatuluka ku zithando zao zankhondo, nkusendera kuti lidzakumane ndi Ayuda. Okwera pa akavalo anali magulu aŵiri; oponya miyala ndiponso amauta ankayenda patsogolo, pamodzi ndi ankhondo onse olimba mtima.

12Bakide anali ndi gulu la ku dzanja lamanja. Ankhondo onse ankayenda mwa magulu ao aŵiri namaliza malipenga.

13Anthu a Yudasi nawonso adaliza malipenga, pansi nkumachita kugwedezeka ndi phokoso la magulu ankhondowo. Nkhondo idalimba kuyambira m'maŵa mpaka madzulo.

14Yudasi ataona kuti Bakide ndi gulu lomthandiza ali mbali ya ku dzanja lamanja, adasonkhanitsa anthu olimba mtima kuti akhale pafupi naye.

15Adapambana gulu lankhondo la adani lakumanja. Adalipirikitsa mpaka ku phiri la Azoto.

16Koma adani a gulu lakumanzere ataona kuti gulu lakumanja lathaŵa, adatembenuka nayamba kulondola Yudasi ndi anthu ake nkumaŵasaka.

17Nkhondo idakula koopsa! Ndipo m'magulu aŵiriwo, ambiri adalasidwa naafa.

18Yudasi nayenso adafa, anthu ake otsala nkuthaŵa.

Maliro a Yudasi Makabeo

19Yonatani ndi Simoni adanyamula mtembo wa mbale wao, nauika m'manda a makolo ao ku Modini.

20Aisraele onse adalira maliro ake kwambiri. Adalira malirowo masiku ambiri.

21Polira ankati,

“Ha, kani yagwa motere ngwazi yamphamvu ija,

mpulumutsi wa Israele!”

22Ntchito zina za Yudasi, nkhondo zake ndi zina zonse zimene adaachita, kudzanso za ukulu wake, sizidalembedwe zonse ai, chifukwa zinali zochuluka kwambiri.

Yonatani akhala mfumu pamalo pa Yudasi

23Yudasi atafa, mudayambanso kuwoneka anthu osiya chipembedzo chao m'dziko lonse la Israele, ndipo onse ochita zoipa adaonekera poyera.

24Masiku amenewo kunali njala yaikulu, ndipo anthu a m'dzikomo adathaŵira kwa adani.

25Tsono Bakide adasankha anthu oletsa chipembedzo, naŵaika kuti akhale olamulira dziko.

26Iwoŵa adayamba kufunafuna abwenzi a Yudasi. Akaŵapeza ankaŵapereka kwa Bakide, ndipo iyeyo ankaŵalipsira ndi kuŵanyazitsa.

27Motero Aisraele anali ndi nkhaŵa yoopsa. Sadaonekepo mavuto otere kuyambira nthaŵi imene aneneri adaleka kuwoneka ku Israele.

28Pamenepo abwenzi ake onse a Yudasi adasonkhana kwa Yonatani, ndipo adamuuza kuti,

29“Momwe adamwalirira mbale wanu Yudasi, palibe munthu wina wofanafana naye pa nkhondo zomenyana ndi Bakide ndi ena onse odana ndi mtundu wathu.

30Tsono takusankhulani inuyo lero kuti mukhale mfumu yathu m'malo mwa iye uja, ndiponso kuti muzititsogolera pa nkhondo zathu.”

31Tsiku limenelo Yonatani adavomera ntchito ya utsogoleri, natenga malo a Yudasi mbale wake.

Amenyana nkhondo ndi Bakide

32Bakide atamva zimenezo, adaganiza zoti aphe Yonatani.

33Yonatani ndi mbale wake Simoni ndi anthu ake onse othandizana naye, atamva zimenezo, adathaŵira ku chipululu cha Tekowa, nkukamanga zithando zao pafupi ndi madzi a chitsime cha ku Asifare.

34(Bakide atamva, adapita ndi ankhondo ake onse pa tsiku la Sabata kutsidya kwa Yordani).

35Yonatani adatuma mbale wake Yohane, amene anali mkulu wa asilikali, kuti akapemphe abwenzi ake Anabate kuti aŵasungire katundu wao amene anali wochuluka.

36Koma ana a Yambiri adatuluka ku Medeba naŵathira nkhondo mwadzidzidzi. Adagwira Yohane nkulanda zonse zimene anali nazo, nabwerera kwao ndi chumacho.

37Pambuyo pake, ena adadziŵitsa Yonatani ndi mbale wake Simoni kuti ana a Yambiri akuchita chikondwerero chachikulu cha ukwati, ndipo kuti atachoka ku Nadabati, ankabwera ndi mkwati wamkazi ndi gulu lalikulu la anthu. Mkwati wamkaziyo anali mwana wa mmodzi mwa akuluakulu otchuka a ku Kanani.

38Pamenepo Ayuda adakumbukira imfa ya mbale wao Yohane, ndipo adakwera ku phiri nakabisala m'mapanga.

39Poti ayang'ane, adaona anthu ambirimbiri ali ndi katundu wambiri. Adaonanso mkwati wamwamuna, abale ake ndi abwenzi ake akudzaŵachingamira ali ndi zida zankhondo ndipo akuimba ting'oma ndi azeze.

40Tsono Ayuda adasokoloka kumene adaabisala, naŵalumphira, nkuyamba kuŵakantha. Ambiri adaphedwa, ndipo otsala adathaŵira ku mapiri. Pamenepo Ayuda adatenga katundu wao yense.

41Choncho chikondwerero cha ukwati chija chidasanduka maliro, ndipo nyimbo zao zidasanduka madandaulo.

42Pakutero Yonatani ndi Simoni adalipsira chifukwa cha imfa ya mbale wao Yohane, kenaka adabwerera ku zigwa za ku Yordani.

43Bakide atamva zimenezi, adadza pa tsiku la Sabata ku gombe la Yordani pamodzi ndi gulu lankhondo.

44Yonatani adauza anthu ake kuti, “Tiyeni tinyamuke tsopano kukamenya nkhondo kuti tipulumutse moyo wathu, lero zinthu sizili monga kale.

45Kutsogoloku kuli adani athu, kumbuyoku kuli Yordani. Kumanja ndi kumanzere kuli mataŵale ndi malunje. Kulibe koti tingathaŵireko.

46Tsopano pempherani kwa Mulungu kuti mupulumuke kwa adaniŵa.” Nkhondo idayambika pomwepo.

47Yonatani adayesetsa kuti akanthe Bakide, koma iye adamlewa pobwerera kumbuyo.

48Tsono Yonatani ndi anthu ake adalumphira mu Yordani. Adasambira naoloka mtsinjewo, koma adani sadaoloke kuti aŵatsate.

49Tsikulo anthu a Bakide adaphedwa pafupi 1,000.

50Bakide atabwerera ku Yerusalemu, adatuma anthu kuti amange malinga olimba ndi nsanja zankhondo ku mizinda ya ku Yudeya, monga ku Yeriko, Emausi, Betoroni, Betele, Timnati, Faratoni ndi ku Tefoni. Konseko adamangitsa malinga aatali ndi zitseko ndi mipiringidzo yake.

51Adaikako maboma ankhondo kuti azilimbana ndi Aisraele.

52Adamangiranso linga mzinda wa Betizure ndi wa Gazara ndi chinyumba chankhondo cha ku Ziyoni, naikako ankhondo ndi chakudya.

53Adagwira ana a anthu otchuka am'dzikomo ngati zikole, naŵatsekera m'chinyumba chankhondo chija ku Yerusalemu.

54Chaka cha 153, pa mwezi wachiŵiri, Alikimo mkulu wa ansembe onse, adalamula kuti agumule khoma la bwalo lam'kati la Nyumba ya Mulungu. Potero ankafuna kuwononga ntchito zonse za aneneri.

55Koma atangoiyamba ntchitoyo, nthaŵi yomweyo Mulungu adamlanga Alikimo, ndipo ntchito yake idalekeka. Mano ake adalumana, ziwalo zidafa, osatha kunena ndi mau amodzi omwe, kapena kulamula kanthu kwa a m'nyumba mwake.

56Pasanapite nthaŵi yaitali Alikimo adamwalira atazunzika kwambiri.

57Bakide ataona kuti Alikimo wamwalira, adabwerera kwa mfumu, ndipo m'dziko la Yudeya mudakhala mtendere zaka ziŵiri.

Nkhondo ina ya Bakide

58Tsono Ayuda okana chipembedzo chao adapangana navomerezana, adati, “Onani, Yonatani ndi anzake ali pa mtendere opanda zovuta. Ndiye tiyeni tiitane Bakide, adzaŵagwire onse usiku umodzi.”

59Motero adapitadi kukamvana naye.

60Bakide adanyamuka ndi gulu lalikulu lankhondo. Anaŵatumizira m'seri makalata abwenzi ake okhala ku Yudeya kuti agwire Yonatani ndi anzake. Koma adalephera kuŵagwira, chifukwa iwowo anali atamva za chiwembu chaocho.

61Pamenepo Yonatani ndi anthu ake adagwira anthu makumi asanu pakati pa anthu am'dzikomo, omwe adaatsogolera anzao pochita chiwembucho, naŵapha.

62Kenaka Yonatani ndi Simoni ndi anthu okhala nawo adapita ku Betibasi ku chipululu, namanganso nyumba zimene zinali zitagumulidwa, ndipo adazilimbitsa ndi malinga.

63Bakide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo ake onse, naitana anthu ena a ku Yudeya.

64Adabwera nkudzamanga zithando zao zankhondo pafupi ndi Betibasi, nazinga mzindawo masiku ambiri ndi makina ankhondo.

65Koma Yonatani adamsiya mbale wake Simoni mumzindamo, napita ku miraga ali ndi gulu laling'ono la ankhondo.

66Kumeneko adagonjetsa Odomera ndi abale ake ndi ana a Fasironi m'mahema mwao. Kenaka adaputa ozinga aja ndi kumenyana nawo.

67Simoninso adatuluka ndi anzake natentha makina ankhondo a adani.

68Aŵiriwo adamenyana ndi Bakide, namgonjetseratu. Tsono iye ataona kuti zolinga zake ndi nkhondo yake zapita pachabe,

69adapsa mtima chifukwa cha anthu okana chipembedzo chao aja, amene adaamlangiza kuti abwere m'dzikomo. Adapha anthu ambiri mwa iwo, nayamba kukonzekera zoti abwerere ku dziko lakwao.

70Yonatani atamva zimenezi adamtumira amithenga kuti apangane naye za mtendere ndi kupempha kuti aŵabwezere anthu amene adaaŵagwira ku nkhondo.

71Bakide adaŵalandira bwino amithengawo, navomera mau a Yonatani. Adamlonjeza molumbira kuti sadzamchitanso zoipa masiku onse a moyo wake.

72Adambwezera anthu amene adaaŵagwira aja, ndipo iye adabwerera kwao, osapondanso dziko la Yuda.

73Motero nkhondo idaleka kuvutanso Aisraele, ndipo Yonatani adakakhala ku Mikimasi. Adayamba kulamulira anthu ake, nachotsa anthu okana chipembedzo pakati pa Aisraele.

Aleksandro Balasi apatsa Yonatani ukulu wa unsembe
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help