Yer. 42 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yeremiya achenjeza Ayuda kuti asathaŵire ku Ejipito

1Atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya, Azariya mwana wa Hesaya, kudzanso anthu onse ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, adapita kwa mneneri Yeremiya. Adamuuza kuti,

2“Ife tabwera ndi dandaulo lathu. Chonde, mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wanu, ife amene tatsala oŵerengeka. Tangotsalatu ochepa chabe pa anthu ambiri, monga mukutiwoneramu.

3Mupemphere kuti Chauta, Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi zimene tikachite.”

4Apo mneneri Yeremiya adaŵauza kuti, “Ndamva zimene mwanenazi, ndidzapemphera kwa Chauta, Mulungu wanu monga mukufunira. Ndipo zonse zimene Chauta Mulungu wanu ati anene, ndidzakuuzani, sindidzakubisirani kanthu.”

5Iwowo adauza Yeremiya kuti, “Chauta akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ngati sitichita zimene Chauta Mulungu wanu wakutumani kuti mudzatiwuze.

6Kaya nzabwino, kaya zoipa, tidzamvera ndithu mau a Chauta Mulungu wathu, amene takutumani kuti mukampemphe kanthu m'dzina lathu. Tidzamvera Chauta Mulungu wathu, kuti zinthu zitiyendere bwino.”

Chauta ayankha pemphero la Yeremiya

7Atatha masiku khumi, Chauta adalankhula ndi Yeremiya.

8Tsono Yeremiya adaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali nawo, ndiponso anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.

9Adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, amene mudaandituma kuti ndikampemphe kanthu m'dzina lanu, akunena kuti,

10‘Ngati mukhala m'dziko lino, ndiye kuti mudzakhazikika, sindidzakuchotsani. Zoonadi, ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani konse. Ndikumva chisoni chifukwa cha mazunzo amene ndidagwetsa pa inu.

11Musaiwope mfumu ya ku Babiloni imene mukuiwopa tsopano. Musaiwope mfumuyo, chifukwa Ine ndili nanu, kuti ndikupulumutseni ndi kukuchotsani m'manja mwake, ndatero Ine Chauta.

12Ndidzakuchitirani chifundo, kotero kuti iyenso adzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale m'dziko lanu lino.’

13Koma mwina simumvera mau a Chauta, nkunena kuti,

14‘Ai, tipita ndithu ku Ejipitoko, kopanda nkhondo, kosamva kulira kwa lipenga, kosasoŵa chakudya, ndipo tidzakhala kumeneko.’

15Tsono mukatero, inu otsala a ku Yuda, imvani mau aŵa a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. Akunena kuti, ‘Mukatsimikiza za kupita ku Ejipitozi, nkupitadi kukakhala kumeneko,

16ndiye kuti nkhondo mukuiwopayo idzakugonjetsani ku Ejipito komweko. Njala mukuiwopayo idzakuvutanibe ngakhale ku Ejipitoko, ndipo mudzafera kumeneko.

17Anthu onse amene akutsimikiza za kupitadi ku Ejipito, ndi kukakhala kumeneko, adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatsale kapena kupulumuka ku zoopsa zimene ndidzaŵagwetsere.’ ”

18“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunenanso kuti, ‘Monga momwe anthu okhala ku Yerusalemu ndidaŵakwiyira mwaukali, momwemonso ndidzakukwiyirani inuyo mukadzapita ku Ejipito. Mudzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chomachiseka ndi chonyozeka. Malo ano simudzaŵaonanso.

19Inu otsala a ku Yuda, musapite ku Ejipito. Ndithudi ndakuchenjezani lero, kusokera kwanu kungakutayitseni moyo.’

20Paja mudaandituma kwa Chauta Mulungu wanu ndi kunena kuti, ‘Mutipempherere kwa Chauta Mulungu wathu, ndipo mutiwuze chilichonse chimene Chauta Mulungu wathu ati anene, ife tidzazichita.’

21Ndakuuzani zonse lero, koma simudamvere Chauta Mulungu wanu pa zonse zimene adandituma kuti ndikuuzeni.

22Tsono mudziŵe kuti mudzafadi ndi nkhondo, njala ndiponso mliri, ku malo amene mufuna kupita kuti mukakhaleko.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help