Gen. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe athaŵa kwa Labani

1Yakobe adamva kuti ana a Labani ankanena kuti, “Yakobe watenga zonse za bambo wathu. Wapeza chuma chake m'chuma cha bambo wathu.”

2Yakobe adazindikiranso kuti Labani sankamuwonetsa nkhope yabwino ngati kale.

3Tsono Chauta adamuuza kuti, “Bwerera ku dziko la atate ako ndi kwa abale ako. Ine ndidzakhala nawe.”

4Tsono Yakobe adatumiza mau kwa Rakele ndi kwa Leya kuti akakumane naye kubusa kumene kunali zoŵeta zake.

5Atafikako, iye adaŵauza kuti, “Ndaona kuti bambo wanu tsopano sakundipenya ndi maso abwino ngati kale. Koma Mulungu wa atate anga wakhala nane.

6Nonse aŵirinu mukudziŵa bwino kuti ndidagwira ntchito kwa bambo wanu ndi mphamvu zanga zonse.

7Komabe iye wandipusitsa, ndipo malipiro anga waasinthasintha kakhumi konse. Koma Mulungu sadamlole kuti andichite choipa.

8Nthaŵi zonse Labani akanena kuti, ‘Zoŵeta zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkakhala zamathothomathotho. Ndipo akanena kuti, ‘Zamipyololo zikhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkangokhala zamipyololo.

9Mulungu watenga zoŵeta zonse kwa bambo wanu, wapatsa ine.

10Pa nthaŵi yakuti zoŵeta zitenga maŵere, ine ndidalota maloto, ndipo ndidaona kuti atonde amene ankakwerawo anali amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga.

11Ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula nane m'maloto momwemo nandiitana kuti, ‘Yakobe,’ ine ndidayankha kuti, ‘Ee Ambuye!’

12Iye adati, ‘Tayang'ana, ndipo upenye kuti atonde onse amene akukweraŵa ndi amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Zimenezi ndachita ndine, popeza kuti ndaona zimene Labani akukuchita.

13 Mulungu wa atate ao, ndiye adzatiweruze ife aŵiri.” Motero Yakobe adalumbira m'dzina la Mulungu amene Isaki bambo wake ankamuwopa.

54Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo.

55M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Labani adampsompsona adzukulu ake aja pamodzi ndi ana ake aakaziwo naŵatsazika, ndipo ataŵadalitsa adachoka namapita kwao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help