1 2Sam. 9.9, 10 Davide atabzola pang'ono pamwamba pa phiri, adakumana ndi Ziba, mtumiki wa Mefiboseti, ali ndi abulu a chishalo pa msana, atasenza buledi wokwanira 200, masangwe a mphesa 100, zipatso zapachilimwe 100, ndiponso thumba la vinyo.
2Mfumu idafunsa Ziba kuti, “Chifukwa chiyani wabwera ndi zimenezi?” Ziba adayankha kuti, “Amfumu, abuluŵa ndi oti anthu a m'banja mwanu azikwerapo. Bulediyu, ndi zipatso zapachilimwezi nzoti ankhondo azidya, ndipo thumba la vinyoli nloti anthu amene azikomoka m'chipululu azimwa.”
32Sam. 19.25-27 Kenaka mfumu idamufunsa kuti, “Nanga mwana wa mbuyako ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Watsalira ku Yerusalemu, poti akunena kuti, ‘Aisraele andibwezera ufumu wa bambo wanga tsopano.’ ”
4Apo mfumu idauza Ziba kuti, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti nzako.” Ziba adati, “Pepani, ndakupembani, mbuyanga mfumu, bwanji nthaŵi zonse ndizipeza kuyanja pamaso panu!”
Davide ndi Simei.5Pamene mfumu Davide adafika ku mzinda wa Bahurimu, kudatulukira munthu wa ku banja la Saulo, dzina lake Simei, mwana wa Gera. Ankabwera akungotukwana.
6Simeiyo ankaponya miyala mfumu Davide ndiponso nduna zake zonse. Nthaŵiyo nkuti atetezi ake ndi ankhondo ake ali kwete kuzungulira mfumuyo.
7Simei potukwanapo ankati, “Choka, choka, iwe munthu wopha anthu, munthu wachabechabe.
8Chauta wakulipsira chifukwa chakuti udapha onse a banja la Saulo, nulanda ufumu wake. Ndipotu Chauta wapereka ufumuwo kwa mwana wako Abisalomu. Ona, kutha kwako nkumeneku, pakuti iweyo ndiwe wopha anthu.”
9Pamenepo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mukulola galu wakufayu kuti akutukwaneni chotere, inu mbuyanga mfumu? Mundilole ndikamdule pa khosi.”
10Koma mfumu idayankha kuti, “Zikukukhudzani bwanji zimenezi, inu ana a Zeruya? Ngati iyeyu akunditukwana chifukwa choti Chauta wachita kumuuza kuti, ‘Mtukwane Davideyu’, ndani angamufunse kuti, ‘Bwanji wachita zimenezi?’
11Tsono Davide adauza Abisai ndi atsogoleri ake kuti, ‘Mwana wanga weniweni akufuna kundipha, nanga nanji Mbenjaminiyu? Mlekeni azitukwana, pakuti wachita kumlamula ndi Chauta kuti atero.
12Mwina mwake Chauta adzaona mavuto anga, nadzandibwezera zabwino chifukwa cha kunditukwanaku.’ ”
13Motero Davide ndi anthu ake ankayenda mu mseu pamene Simei ankapita mbali inai m'mphepete mwa phiri, kutukwana kuli m'kati. Ndipo ankaponya miyala Davide ndi kumamuwazanso dothi.
14Tsono mfumu ndi anthu onse amene anali naye, adafika ku Yordani ali otopa kwambiri, napumula kumeneko.
Abisalomu aloŵa mu Yerusalemu.15Abisalomu ndi Aisraele onse amene anali naye, kudzanso Ahitofele, adaaloŵa mu Yerusalemu.
16Ndipo pamene Husai Mwariki, bwenzi la Davide, adakumana ndi Abisalomu, adafuula kwa Abisalomuyo kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali! Amfumu akhale ndi moyo wautali!”
17Tsono Abisalomu adafunsa Husai kuti, “Kodi ndimo m'mene umamkondera bwenzi lako? Chifukwa chiyani sudapite naye limodzi bwenzi lakoyo?”
18Apo Husai adayankha Abisalomu kuti, “Iyai, munthu amene wasankhidwa ndi Chauta ndiponso ndi anthu aŵa, kudzanso amuna onse a Aisraele, ndiye ndidzakhale mtumiki wake, ndipo ndidzakhala pambuyo pake.
19Nanganso ndani amene ine ndingamtumikire? Kodi si inuyo mwana wa mfumu? Monga momwe ndidatumikira bambo wanu, momwemonso ndidzakutumikirani inu.”
20Tsono Abisalomu adafunsa Ahitofele kuti, “Iwe ukuganiza bwanji pamenepa? Tsopano tichite chiyani?”
21Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Pitani mukaloŵe kwa azikazi a bambo wanu amene adaŵasiya kuti azisunga mudzi. Aisraele onse akadziŵa kuti bambo wanu akuipidwa nanu, onse amene akukutsataniŵa adzalimba mtima.”
222Sam. 12.11, 12 Motero adamangira Abisalomu hema pa denga la nyumba ya mfumu. Ndipo Abisalomu adapita kukaloŵa kwa azikazi a bambo wake, Aisraele onse akupenya.
23Tsono masiku amenewo, malangizo amene ankapereka Ahitofele anali ngati mau ochokera kwa Mulungu. Choncho uphungu wonse wa Ahitofele ankaulemekeza Davide ndi Abisalomu yemwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.