1Yosiya adachita Paska ku Yerusalemu, kuchitira Chauta. Adapha mwanawankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.
2Adaika ansembe pa maudindo ao, namaŵalimbitsa mtima pa ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta.
3Pambuyo pake adauza Alevi onse amene ankaphunzitsa Aisraele ndipo anali opatulikira Chauta, kuti, “Muike bokosi lopatulika m'Nyumba imene Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele, adamanga. Simuzidzalisenzanso pa mapewa anu ai.
42Mbi. 8.14 Mugaŵikane m'magulu malinga ndi mabanja anu, potsata zimene adalemba Davide mfumu ya Israele ndi zimene adalemba Solomoni mwana wake.
5Muziimirira ku malo opatulika potsata magulu a mabanja a abale anu amene sali ansembe. Ndipo banja lililonse la Alevi likhale ndi chigawo chake.
6Tsono muphe mwanawankhosa wa Paska, ndipo mudziyeretse. Muthandize abale anu, kuti zipherezere zimene Chauta adalankhula kudzera mwa Mose.”
7Tsono Yosiya adapereka kwa anthu wamba anaankhosa ndi anaambuzi okwanira 30,000 ndiponso ng'ombe zamphongo 3,000, zopereka za Paska. Zimenezi adazitenga pa chuma cha mfumu.
8Nduna zakenso zidapereka mwaufulu kwa anthu, kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a ku Nyumba ya Mulungu, adapereka kwa ansembe zopereka izi za Paska: anaankhosa ndi anaambuzi 2,600, ndiponso ng'ombe zamphongo 300.
9Konaniya nayenso, Semaya ndi Netanele, abale ake, pamodzi ndi Hasabiya, Yeiyele ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, adapereka kwa Alevi zopereka izi za Paska: anaankhosa ndi anaambuzi 5,000, ndiponso ng'ombe zamphongo 500.
10Zonse zidayenda bwino malinga ndi mwambo wake: ansembe adakaima ku malo ao ndipo Alevi adakakhala m'magulu mwao, potsata ulamuliro wa mfumu.
11Ndipo adapha mwanawankhosa wa Paska. Tsono ansembe adawaza magazi amene adaŵalandira kwa Alevi, pamenepo nkuti Aleviwo akusenda nyamazo.
12Adapatula nsembe zopsereza, kuti azipereke potsata magulu a mabanja a anthu wamba, pamene ankapereka zao kwa Chauta, monga momwe zidaalembedwera m'buku la Mose. Ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi ng'ombe zija.
13Eks. 12.8, 9 Tsono adaotcha mwanawankhosa wa Paska pa moto, potsata mwambo. Adaphika nyama yamwanawankhosa ya Paska m'mbiya, m'mitsuko ndi m'ziwaya. Ndipo adazipereka mofulumira kwa anthu osakhala ansembe.
14Pambuyo pake ankakonza zao ndi za ansembe, chifukwa chakuti ansembe, ana a Aaroni, anali otanganidwa ndi kupereka nsembe zopsereza ndi kutentha mafuta mpaka usiku. Choncho Alevi ankakonza zao ndiponso za ansembe, ana a Aaroni.
151Mbi. 25.1 Anthu oimba nyimbo, ana a Asafu, anali atakhala m'malo mwao potsata lamulo la Davide, la Asafu, la Hemani ndi la Yedutuni, mneneri wa mfumu. Alonda apazipata anali ku chipata chilichonse. Choncho kunali kosafunika kuti achokepo pa ntchito yao, poti abale ao Alevi ankaŵakonzera zonse.
16Motero ntchito zonse za Chauta zidakonzeka tsiku limenelo, kuti anthu achite Paska ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la Chauta, potsata lamulo la mfumu Yosiya.
17Eks. 12.1-20 Choncho Aisraele amene anali pamenepo adachita Paska nthaŵi imeneyo, ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa.
18Sidachitikepo Paska yofanafana ndi imeneyi ku Israele chiyambire nthaŵi ya Samuele, mneneri uja. Panalibe ndi imodzi yomwe mwa mafumu a Aisraele imene idachitapo Paska monga imene adachita Yosiya, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, Ayuda ndi Aisraele onse amene analipo, kudzanso nzika za mu Yerusalemu.
19Adachita Paska imeneyi pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yosiya.
Yosiya amenya nkhondo ndi mfumu Neko wa ku Ejipito(2 Maf. 23.28-30)20Zitapita zimenezi ndipo Yosiya atakonza Nyumba ya Chauta, Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukamenya nkhondo ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya adapita kukamenyana naye.
21Koma Neko adatuma amithenga kwa iyeyo kukamufunsa kuti, “Kodi iwe mfumu ya ku Yuda, ukuti tichitane chiyani? Ine sindibwera kudzalimbana ndi iwe lero, koma ndidzalimbana ndi banja limene ndikumenyana nalo nkhondo. Ndipo Mulungu wandilamula kuti ndifulumire. Siya kukangana ndi Mulungu amene ali nane, kuwopa kuti angakuwononge.”
22Koma Yosiya sadachoke ndipo adadzizimbaitsa kuti amenyane naye nkhondo. Sadasamale mau a Nekoyo amene Mulungu adaalankhula, koma adakamenyana ku chigwa cha Megido.
23Ndipo anthu oponya mivi adamlasa mfumu Yosiya. Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, “Chotseni, poti ndalasidwa koipa.”
24Anyamata akewo adamchotsa pa galetalo namkweza pa galeta lake lachiŵiri, napita naye ku Yerusalemu. Ndipo adafa, naikidwa m'manda a makolo ake. Anthu onse a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adamulira Yosiya.
25Yeremiya nayenso adapeka nyimbo yamaliro chifukwa cha Yosiyayo. Anthu onse oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, akhala akunena za Yosiya pomlira mpaka lero lino. Zimenezi zakhala ngati mwambo ku Israele, ndipo zidalembedwa m'buku lotchedwa “Madandaulo.”
26Tsono ntchito zina zonse za Yosiya ndi ntchito zake zabwino zimene adazichita, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a Chauta,
27ntchito zake zoyamba ndi zomalizira, zonsezo zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.