1Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake
ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
2pali nthaŵi yobadwa
ndi nthaŵi yomwalira,
pali nthaŵi yobzala
ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
3Pali nthaŵi yakupha
ndi nthaŵi yochiritsa,
nthaŵi yogwetsa
ndi nthaŵi yomanga.
4Pali nthaŵi yomva chisoni
ndi nthaŵi yosangalala,
nthaŵi yolira maliro
ndi nthaŵi yovina.
5Pali nthaŵi yokhala malo amodzi
ndi nthaŵi yotalikirana,
nthaŵi yokumbatirana
ndi nthaŵi yoleka zokumbatiranazo.
6Pali nthaŵi yofunafuna
ndi nthaŵi yotaya,
nthaŵi yosunga
ndi nthaŵi yomwaza.
7Pali nthaŵi yong'amba
ndi nthaŵi yosoka,
nthaŵi yokhala chete
ndi nthaŵi yolankhula.
8Pali nthaŵi yokondana
ndi nthaŵi yodana,
nthaŵi ya nkhondo
ndi nthaŵi ya mtendere.
9Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa?
10Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira.
11Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira.
12Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao.
13Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
14Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera.
15Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso.
Pa dziko lapansi palibe chilungamo16China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa.
17Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.”
18Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama.
19Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake.
20Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.
21Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka?
22Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.