Mt. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za tsiku la Sabata(Mk. 2.23-28; Lk. 6.1-5)

1 Deut. 23.25 Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake anali ndi njala, ndipo adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya.

2Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.”

31Sam. 21.1-6Iye adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala?

4Lev. 24.9 Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo kunali kosaloledwa kuti iyeyo kapena anzakewo nkumudya, koma ansembe okha.

5Num. 28.9, 10Kaya simudaŵerengenso m'Malamulowo kuti m'Nyumba ya Mulungu, pa tsiku la Sabata, ansembe amaphwanya lamulo lokhudza tsiku la Sabata, komabe saŵayesa olakwa?

6Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo.

7Mt. 9.13; Hos. 6.6 Mukadadziŵa tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai,’ sibwenzi mutaweruza kuti ndi olakwa anthu amene sadalakwe konse.

8Pajatu Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”

Yesu achiritsa munthu wopuwala dzanja(Mk. 3.1-6; Lk. 6.6-11)

9Yesu adachoka kumeneko nakaloŵa m'Nyumba yamapemphero.

10M'menemo munali munthu wopuwala dzanja. Tsono anthu ena amene ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, adamufunsa kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata?”

11Lk. 14.5Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa?

12Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”

13Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake.

14Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu.

Yesu, mtumiki wosankhidwa wa Mulungu

15Yesu atamva za upowo, adachokako kumeneko. Anthu ambiri adamtsatira, ndipo Iye adaŵachiritsa onse amene ankadwala.

16Koma adaŵalamula kuti asakamuulule.

17Adaachita zimenezi kuti zipherezere zimene Mulungu adaalankhulitsa mneneri Yesaya kuti,

18 Yes. 42.1-4 “Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha.

Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri.

Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo,

ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina.

19Iye sadzachita makani, kapena kufuula.

Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda.

20Iye sadzatsiriza bango lothyoka,

nyale yofuka sadzaizimitsa,

mpaka atapambanitsa chilungamo.

21Ndipo anthu akunja adzamdalira.”

Za Yesu ndi Belezebulu(Mk. 3.2-30; Lk. 11.14-23; 12.10)

22Pambuyo pake anthu adadza kwa Yesu ndi munthu wakhungu, wosatha kulankhula, ndi woloŵedwa mizimu yoipa. Tsono Yesu adamchiritsa, kotero kuti adayamba kulankhula ndi kupenya.

23Anthu onse adazizwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?”

24Mt. 9.34; 10.25Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.”

25Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.

26Ngati a mu ufumu wa Satana atulutsana okhaokha, ndiye kuti agaŵikana. Nanga Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji?

27Inu mukuti Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzeni kuti ndinu olakwa.

28Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.

29 Tob. 8.3 “Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo.

30 Mk. 9.40 “Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.

31Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira.

32Lk. 12.10Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”

Za mtengo ndi zipatso zake(Lk. 6.43-45)

33 Mphu. 27.6; Mt. 7.20; Lk. 6.44 “Mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwabwino,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzabwino. Koma mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwoipa,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzoipa. Pajatu mtengo umadziŵika ndi zipatso zake.

34Mt. 3.7; 23.33; Lk. 3.7; Mt. 15.18; Lk. 6.45Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.

35Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake.

36Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.

37Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Anthu apempha chizindikiro chozizwitsa(Mk. 8.11-12; Lk. 11.29-32)

38 Mt. 16.1; Mk. 8.11; Lk. 11.16 Pamenepo aphunzitsi ena a Malamulo ndi Afarisi ena adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tifuna kuti mutiwonetse chizindikiro chozizwitsa.”

39Mt. 16.4; Mk. 8.12 Koma Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ndi oipa ndi osakhulupirika, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija.

40Yon. 1.17Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku.

41Yon. 3.5 Pa tsiku la chiweruzo anthu a ku Ninive adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.

421Maf. 10.1-10; 2Mbi. 9.1-12 Pa tsiku la chiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.”

Za mzimu woipa wobwerera mwa munthu(Lk. 11.24-26)

43“Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako, koma osaŵapeza.

44Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino.

45Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.”

Amai ake ndi abale ake a Yesu(Mk. 3.31-35; Lk. 8.19-21)

46Pamene Yesu ankalankhula ndi anthu ambirimbiri aja, nthaŵi yomweyo amai ake ndi abale ake adafika, naima panja. Ankafuna mpata woti alankhule naye.

47Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kulankhula nanu.”

48Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ine amai anga ndani? Ndipo abale anga ndani?”

49Atatero, adaloza ophunzira ake nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa.

50Pakuti aliyense wochita zimene Atate anga akumwamba akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help