1Zonsezi zitatha, Aisraele onse amene analipo adapita ku mizinda ya Yuda, nakaphwanyaphwanya zipilala, kugwetsa mafano, ndi kuwononga akachisi ndiponso maguwa ku dziko lonse la Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase, mpaka kuwonongeratu zonse. Pambuyo pake Aisraele onse adabwereranso kumapita kumizinda kwao, aliyense ku dziko lake.
2Hezekiya adakhazikitsanso magulu a ansembe ndi a Alevi, gulu lililonse kutsata ntchito yake. Ansembe ndi Aleviwo ena adaŵaika kuti azipereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, ena kumatumikira ku zipata za bwalo la Chauta, ena kumathokoza ndi kutamanda.
3 za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse.
6Aisraele ndi Ayuda amene ankakhala ku mizinda ya Yuda, ankabwera ndi zigawo zachikhumi za ng'ombe ndi nkhosa, ndiponso zinthu zopatulika zimene anali atazipereka kwa Chauta, Mulungu wao, namaziika zonsezo m'milum'milu.
7Adayamba kumaunjika milu pa mwezi wachitatu natsiriza pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri.
8Tsono Hezekiya ndi nduna zake atabwera naona miluyo, adatamanda Chauta pamodzi ndi Aisraele anthu ao.
9Hezekiyayo adafunsa ansembe ndi Alevi za milu ija.
10Azariya mkulu wa ansembe amene anali wa m'banja la Zadoki, adamuyankha kuti, “Chiyambire chake cha kupereka zopereka zao ku Nyumba ya Chauta, takhala ndi zinthu zambiri zakudya, ndipo zotsalanso nzambiri. Pakutitu Chauta wadalitsa anthuwo, kotero kuti tili nazo zambirimbiri zotsalazi.”
11Tsono Hezekiya adaŵalamula anthuwo kuti akonze zipinda za ku Nyumba ya Chauta. Iwo adakonzadi zipindazo.
12Pambuyo pake adabwera nazo zoperekazo mokhulupirika, zigawo zachikhumi ndiponso zinthu zopatulika. Tsono kapitao wamkulu woŵayang'anira anali Konaniya Mlevi, pamodzi ndi Simei mbale wake, amene anali wachiŵiri.
13Yehiyele, Azariya, Nahati, Asahele, Yerimoti, Yozabadi, Eliyele, Isiimakiya, Mahati, ndi Benaya, ndiwo amene anali akapitao othandiza Konaniya ndi Simei mbale wake. Mfumu Hezekiya ndiye amene adaŵasankha, pamodzi ndi Azariya amene anali kapitao wamkulu wa ku Nyumba ya Chauta.
14Ndipo Kore, mwana wa Imina Mlevi, amene ankalonda pa chipata chakuvuma ndiye ankayang'anira nsembe zaulere zopereka kwa Mulungu. Ankapatula chigawo cha zopereka choyenera Chauta ndiponso zopereka zoyera kopambana.
15Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, ndiwo amene ankamthandiza mokhulupirika ku mizinda ya ansembe, popereka magawo a zopereka kwa abale ao, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, molingana ndi magulu ao.
16Komanso ankapereka kwa anthu olembedwa potsata mabanja a anthu, ndiye kuti amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka kupitirirapo, amene ankaloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti azigwira ntchito yofunika pa tsiku lake, malinga ndi nthaŵi yao ndi magulu ao.
17Ansembe ankaŵalemba potsata mabanja a makolo ao. Alevi ankaŵalemba kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mtundu wa ntchito yao ndi magulu ao.
18Ansembe adalembedwa pamodzi ndi ana ao onse akhanda, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, kungoti onse a m'banja mwao, chifukwa anali oyenera kudziyeretsa mokhulupirika.
19Kunena za ansembe, ana a Aaroni amene ankakhala ku madera okhala ndi mabusa a mizinda yao, panali amuna ena m'mizinda yoŵerengeka, amene adaauzidwa pakuŵatchula maina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pa ansembewo, ndiponso kwa aliyense pakati pa Alevi amene adalembedwa.
20Hezekiya adachita zimenezi ku dziko lonse la Yuda. Motero adachita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Chauta, Mulungu wake.
21Ntchito iliyonse imene ankachita potumikira ku Nyumba ya Chauta potsata malangizo ndi malamulo, ndi pofunafuna Mulungu wake, ankachita zimenezo ndi mtima wake wonse ndipo ankapeza mwai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.